Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
M’nthawi ino ya masiku otsiriza a dziko loipali, m’pofunika kuvalabe zovala zathu zauzimu ndi kuteteza makhalidwe athu achikristu. (Chiv. 16:15) N’chifukwa chake mutu wa pulogalamu ya msonkhano wadera wa chaka cha utumiki cha 2006 wakuti ‘Valani Umunthu Watsopano’ uli woyenerera.—Akol. 3:10.
Tsiku Loyamba: Nkhani yoyamba yosiyirana yakuti “Kusonyeza Mbali za Umunthu Watsopano,” idzafotokoza mmene kukhala ndi umunthu watsopano kumatipindulitsira m’mbali zonse za moyo wathu. Koma kodi timatani kuti tikhale ndi umunthu watsopanowo? Mbali imeneyi idzafotokozedwa m’nkhani ziwiri zomalizira za tsiku loyambali zakuti “M’pofunika Kudziletsa Kuti Muzisinkhasinkha Bwino” ndi “Maphunziro Amene Amaumba Umunthu Watsopano.”
Tsiku Lachiwiri: Nkhani yakuti “Khalani ndi Lilime la Anzeru” idzafotokoza mmene umunthu watsopano umatithandizira kugwiritsa ntchito bwino lilime lathu. Nkhani ya onse imene idzafotokoza kufunika kokhalabe tcheru ndi machenjera a Satana ili ndi mutu wakuti “Kodi Mukugonjetsa Woipayo?” Nkhani ziwiri zomalizira pa msonkhanowu zakuti, “Khalani Osachitidwa Mawanga ndi Dzikoli” ndi “Kukonza Umunthu Wathu Wam’kati Tsiku ndi Tsiku,” zidzatithandiza kupewa maganizo ndi makhalidwe amene amasemphana ndi njira zolungama za Mulungu ndiponso kuti tikhale olimba pamene tikupembedza Yehova.
Tikudikirira kuti tidzalimbikitsidwe kuvala umunthu watsopano umenewu ndi kusauvulanso.