Lengezani Ulemerero wa Yehova
1 Wamasalmo analengeza kuti: “Myimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi. . . . Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu; zodabwiza zake mwa mitundu yonse ya anthu.” Tikamaganizira zimene Yehova wachita, zimene akuchita, ndi zimene ati adzatichitire, mitima yathu imatisonkhezera kulengeza ulemerero wake!—Sal. 96:1, 3.
2 Mu Utumiki Wathu: Mboni za Yehova zili ndi mwayi wogwiritsa ntchito dzina la Mulungu ndi kulitamanda pamaso pa anthu onse a padziko lapansi. (Mal. 1:11) Zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi atsogoleri a Matchalitchi Achikristu amene modzikuza, achotsa dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo! Pachifukwa chakuti anthu ayenera kuitanira pa dzina limeneli ndi chikhulupiriro kuti adzapulumuke pa chisautso chachikulu chimene chikubwera, ntchito youza anthu dzina la Mulungu imeneyi ndi yofunika kwambiri. (Aroma 10:13-15) Ndiponso, mtendere wa m’chilengedwe chonse, kuphatikizapo mtendere pakati pa anthu, ukudalira kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu. Indedi, zochita zonse za Mulungu zikukhudzana ndi dzina lake.
3 “Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu.” Koma kuti anthu apatse “Yehova ulemerero wa dzina lake,” ayenera kudziwa zoona zenizeni za iye. (Sal. 96:4, 8) Komabe, ena amatsutsa kuti kulibe Mulungu. (Sal. 14:1) Ena amamunyoza kuti alibe mphamvu, kapena amati iye alibe nazo chidwi zochita za anthu. Pamene tikuthandiza anthu oona mtima kuti adziwe molondola Mlengi wathu, zolinga zake, ndi makhalidwe ake abwino, timakhala tikulemekeza Yehova.
4 mwa Khalidwe Lathu: Kutsatira miyezo yolungama ya Yehova kumapereka ulemu kwa iye. Khalidwe lathu labwino limaonekera kwa anthu. (1 Pet. 2:12) Mwachitsanzo, ngati tili anthu aukhondo ndi audongo zingapangitse anthu ena kunena zinthu zabwino zokhudza ifeyo, zimene zingapereke mwayi wakuti tilankhule za ubwino wotsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu. (1 Tim. 2:9, 10) Zimakhala zosangalatsa kwambiri kuona kuti anthu ena ‘pakuona ntchito zathu zabwino, amalemekeza Atate wathu wa Kumwamba’!—Mat. 5:16.
5 Tiyeni titamande Mulungu wathu wolemekezekayo tsiku lililonse mwa zimene timalankhula ndi kuchita. Tikatero, ndiye kuti tikumvera mfuwu ya chisangalalo yakuti: “Myimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.”—Sal. 96:2.