Kulitsani Zizolowezi Zabwino Ndipo Mudzapindula Kwambiri
1. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuonanso zizolowezi zathu zauzimu?
1 N’zosakayikitsa kuti mutangobatizidwa kumene, munachita khama ndi zinthu zauzimu, monga phunziro la Baibulo, misonkhano yachikristu, utumiki wa kumunda, ndi pemphero. Chifukwa chakuti Yehova anadalitsa khama lanu, munakula mwauzimu. Mwina pofika lero, zaka zambiri ndithu zadutsa kuchokera pamene munabatizidwa. Kodi mukupitirizabe kutsatira zizolowezi zabwino zauzimu zimene munali nazo pamene munkakhala Mkristu?
2. Kodi timapindula motani tikamawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku?
2 Onaninso Bwino Zinthu Zimene Munazolowera Kuchita: Kodi muli n’chizolowezi chowerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku? Kuchita zimenezi kumadzetsa madalitso osawerengeka. (Yos. 1:8; Sal. 1:2, 3) Mu Israyeli wakale, mfumu iliyonse inkafunikira kuwerenga buku lake la Chilamulo “masiku onse a moyo wake.” Kodi zimenezi zinali ndi phindu lotani? Kuti mtima wake usadzikuze koma kuti iphunzire kuopa Yehova kuti isasiye malamulo Ake. (Deut. 17:18-20) N’chimodzimodzinso masiku ano, kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kumatithandiza kuti tipitirizebe kukhala oongoka mtima ndi osachitidwa mawanga ndi dziko loipa ndi lachinyengoli. Kumatithandizanso kukhala okonzekera bwino kuchita utumiki wathu.—Afil. 2:15; 2 Tim. 3:17.
3. Kodi timapeza phindu lotani tikamapezeka pamisonkhano nthawi zonse?
3 Yesu anali ndi chizolowezi chopita ku sunagoge, komwe Malemba ankafotokozedwa. (Luka 4:16) Mosakayikira, zimenezi zinam’thandiza kuti asabwerere m’mbuyo pa mavuto amene anakumana nawo patsogolo pake. Ifenso timalimbikitsidwa tikamalandira malangizo auzimu pa misonkhano ya mpingo komanso ‘tikamatothozana.’ (Aroma 1:12) Kusonkhana pamodzi ndi abale athu kumatithandiza kupirira mavuto a m’masiku omaliza ano. (Aheb. 10:24, 25) Kodi muli nachobe chizolowezi chimenechi chopita ku misonkhano yonse?
4. Kodi timapindula motani tikamachita utumiki wa kumunda mlungu ndi mlungu?
4 Baibulo limatiuza kuti atumwi ankalalikira uthenga wabwino “masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba.” (Mac. 5:42) Ngakhale kuti sitingathe kulalikira tsiku lililonse, kodi tingathe kumatenga nawo mbali mu utumiki winawake mlungu uliwonse? N’zosachita kukayikira kuti kuchita zimenezi kungatithandize kukhala aluso pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, ndipo tidzakhala ndi zokumana nazo zabwino pamene tikulalikira choonadi cha m’Baibulo kwa ena.
5. Kodi n’chifukwa chiyani kupemphera kwa Yehova nthawi zonse kuli kofunika?
5 Mneneri Danieli anadalitsidwa kwambiri chifukwa chotumikira Yehova “kosalekeza” moyo wake wonse. Izi zinaphatikizapo chizolowezi chopemphera kwa Yehova. (Dan. 6:10, 16, 20) Ifenso, Yehova angatidalitse ndi mzimu wake woyera tikamapemphera nthawi zonse kwa Iye ndi mtima wathu wonse. (Luka 11:9-13) Koposa zonse, Yehova adzayandikana nafe, n’kutilola kuti tikhale mabwenzi ake a pamtima. (Sal. 25:14; Yak. 4:8) Awa ndi madalitso aakulu kwambiri! Ndiyetu tiyeni tikulitse zizolowezi zathu za zinthu zauzimu ndipo Yehova adzatidalitsa kwambiri.