Sonyezani Ena Chidwi mwa Kulalikira Mopanda Tsankho
1 M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona mngelo akuuluka pakati pa m’mlengalenga, akulalikira uthenga wabwino wosatha “kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chiv. 14:6) Kodi ifenso timalalikira mopanda tsankho monga mngeloyu? N’zotheka kuti mosadziwa tikhale ndi maganizo a tsankho. Mmene timawaonera anthu amene timakumana nawo zimakhudzana kwambiri ndi mmene timalalikirira uthenga wabwino. N’chifukwa chake tifunikira kusonyeza chikondi chenicheni tikamalalikira anthu amene moyo wawo ndi kakulidwe kawo n’kosiyana ndi kathu.
2 Ganizirani Gawo Lanu: Kodi m’gawo lanu muli anthu ochokera ku mayiko ena, kapena amene athawa kwawo pazifukwa zosiyanasiyana? N’zosavuta kuwanyalanyaza anthu amenewa. Yambani ndinu kufufuza anthu amenewa ndipo yesetsani kudziwana nawo bwino. Kodi amasowa zinthu zotani ndipo n’zinthu ziti zimene zimawadetsa nkhawa? Kodi amakonda zinthu zotani ndipo amadana ndi zinthu zotani? Komanso, kodi amaopa chiyani ndipo amakhulupirira zinthu zotani? Yesetsani kugwirizanitsa uthenga wanu wa Ufumu ndi zinthu zimenezo. (1 Akor. 9:19-23) Monga mmene ankachitira mtumwi Paulo, nafenso tiyenera kumva kuti tili ndi udindo wolalikira uthenga wabwino kwa munthu wina aliyense wopezeka m’gawo lathu, kuphatikizapo anthu ochokera ku mayiko ena, a chikhalidwe china, olankhula chinenero china, ndi anthu olemera kwambiri.—Aroma 1:14.
3 Komano, kodi mungalalikire motani munthu amene amalankhula chinenero china? Gwiritsani ntchito bwino kabuku kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu Amitundu Yonse. Mungathenso kumayenda ndi timapepala kapena timabuku ta zinenero zimene zimalankhulidwa kawirikawiri m’gawo lanu. Kuwonjezera pa zimenezi, ofalitsa ena achita khama kuphunzira kupereka moni ndi kulalikira mwachidule chabe m’zinenero zina. Nthawi zambiri anthu amasangalala kumva munthu wina akuyesetsa kulankhula nawo m’chinenero chawo, ngakhale atakhala kuti sakudziwa mawu ambiri, ndipo zimenezi zimatha kuwachititsa kuti amvetsere uthenga wabwino.
4 Tsanzirani Yehova: Tikamayesetsa kulalikira kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana, timakhala tikutsanzira Mulungu wathu wopanda tsankho, Yehova, ‘amene akufuna kuti anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.’—1 Tim. 2:3, 4.