“Kodi Mungayankhe Bwanji?”
1. Kodi ambirife timakhala ndi mavuto otani?
1 Kodi mumakonda Mawu a Mulungu koma n’kulephera kukumbukira bwinobwino nkhani za m’Baibulo kapena pamene mawu enaake amapezeka m’Malemba? Kodi mumafuna kuti ana anu amvetse bwino mfundo ndi ziphunzitso zofunika kwambiri za Baibulo? Mbali yakuti “Kodi Mungayankhe Bwanji?” yomwe imatuluka mwezi ndi mwezi pa tsamba 31, m’magazini ya Galamukani! ingathandize ana ndi akulu omwe kudziwa bwino Mawu a Mulungu.—Mac. 17:11.
2. Kodi zigawo zosiyanasiyana za mbali yakuti “Kodi Mungayankhe Bwanji?” zingagwiritsidwe ntchito motani?
2 Kodi mungatani kuti mupindule ndi mbali imeneyi? Galamukani! ya January 2006 inapereka malingaliro otsatirawa: “Taonani kwa nthawi yochepa chabe zimene zili patsamba 31 . . . Ana azisangalala ndi zigawo zina za tsambali; zina n’zofuna anthu omwe aphunzira Baibulo mozama. Chigawo chakuti ‘Zinachitika Liti?’ chikuthandizani kukhala ndi chithunzithunzi cha nthawi yomwe anthu otchulidwa m’Baibulo anakhala moyo ndiponso nthawi imene zinthu zikuluzikulu zinachitika. Ngakhale kuti mayankho a chigawo chakuti ‘Za M’magazini Ino’ azipezeka m’masamba osiyanasiyana m’magaziniyo, mayankho a mafunso enawo azisindikizidwa mozondotsa patsamba la m’magazini yomweyo, ndipo tizitchula tsamba lake. Bwanji osayamba mwafufuza kaye musanaone mayankho akewo ndipo kenako n’kufotokozera anzanu zimene mwaphunzira? Mungathenso kumakambirana pabanja panu kapena ndi ophunzira Baibulo anzanu, zinthu za patsamba limeneli lakuti, ‘Kodi Mungayankhe Bwanji?’”
3. Kodi mabanja ena apindula motani ndi mbali imeneyi, ndipo inuyo mumakonda kwambiri zigawo ziti?
3 N’zoona kuti mabanja ambiri amasangalala kugwiritsa ntchito mbali imeneyi pa phunziro lawo la banja. Mayi wina analemba kuti: “Ine ndi mwamuna wanga tinaona kuti zingakhale bwino kuti pa phunziro lathu la banja tiziphatikizapo chigawo chakuti ‘Zithunzi Zoti Ana Apeze’ n’cholinga choti phunzirolo lizikhala losangalatsa ndi lochititsa chidwi kwa mwana wathu wamkazi wa zaka zitatu. Timasangalala kwambiri tikamamuona akutsegula mokondwa masamba osiyanasiyana m’magazini yake ya Galamukani! kufufuza chithunzi chimene akufuna, mpaka atachipeza.” Bambo wina wa ku Brazil anati: “Ine ndi mwana wanga wamwamuna wa zaka 7 timaikonda kwambiri mbali ya Galamukani! imeneyi. Mbaliyi yathandiza Moises kukhala watcheru, kupeza mavesi m’Baibulo, kudziwa tanthauzo la zithunzi, ndiponso kudziwa zaka zimene zinthu zinachitika.” Ashley, yemwe ndi mtsikana wazaka 8, analemba kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa cha mbali ya ‘Kodi Mungayankhe Bwanji?’ yomwe ikupezeka kumapeto kwa magazini a Galamukani! Mbaliyi imandiphunzitsa zambiri za Baibulo.”
4. Kodi mbali yakuti “Kodi Mungayankhe Bwanji?” ingagwiritsidwe ntchito motani pa phunziro la Baibulo la banja?
4 Konzani zoti nthawi zina pa phunziro lanu la banja muzigwiritsa ntchito mbali ya “Kodi Mungayankhe Bwanji?” Mungathe kugwiritsa ntchito Index kapena Watchtower Library ya pa CD-ROM pofufuza mayankho a ena mwa mafunso ovuta kwambiri. Mukamachita zimenezi, ana anu angaphunzire mmene angafufuzire zinthu. Ngati ana anu ndi osinkhukirapo, bwanji osawauza kuti afufuziretu mayankho a mafunso ovuta a chigawo chakuti “Ndine Ndani?” kapena “Zinachitika Liti?” nthawi ya phunziro la banja isanakwane? Kenako angafotokoze zimene apezazo panthawi ya phunzirolo. Njira imodzi imene makolo angakhomerezere Mawu a Mulungu m’mitima ya ana awo ndi yogwiritsa ntchito bwino tsamba limeneli. Kuchita zimenezi kungathandize anawo kudziwa “malemba opatulika” kuyambira ali akhanda.—2 Tim. 3:15; Deut. 6:7.