Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 April tsamba 2
  • Nkhani Zatsopano Zothandiza Poyamba Kukambirana ndi Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhani Zatsopano Zothandiza Poyamba Kukambirana ndi Anthu
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MMENE TINGAGWIRITSIRE NTCHITO NKHANIZI:
  • Kukambirana Nkhani Zauzimu Kumalimbikitsa
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Tingayambe Bwanji Kukambirana ndi Anthu Pogwiritsa Ntchito Timapepala?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • (1) Funso, (2) Lemba, ndi (3) Mutu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Fotokozani Nkhani Imodzi, Koma Asiyireni Magazini Awiri
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 April tsamba 2

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Nkhani Zatsopano Zothandiza Poyamba Kukambirana ndi Anthu

Duwa lili pachiliza

Kuyambira January 2016, tsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda yogawira likumakhala ndi nkhani yakuti “Kodi Baibulo Limanena Zotani?” Cholinga cha nkhani zimenezi n’kutithandiza kuyamba kukambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Nkhanizi zikumalembedwa mofanana ndi timapepala. Zikumakhala ndi funso lothandiza munthu kufotokoza maganizo ake, yankho la m’Malemba la funsolo komanso mfundo zowonjezera zomwe tingathe kukambirana ndi munthu.

Nthawi zambiri, anthu omwe takambirana nawo bwino mfundo za m’Malemba amayamba kuphunzira Baibulo. Tikukulimbikitsani kuti muzigwiritsa ntchito nkhani zatsopanozi kuti muthandize anthu ambiri omwe akufunafuna choonadi.—Mat. 5:6.

MMENE TINGAGWIRITSIRE NTCHITO NKHANIZI:

  1. Pemphani munthu amene mukumulalikira kuti afotokoze maganizo ake pa funso limodzi

  2. Mvetserani yankho lake ndipo muyamikireni

  3. Werengani lemba lomwe lili pakamutu kakuti “Zimene Baibulo Limanena.” Ndiyeno m’pempheni kuti afotokoze maganizo ake palembalo. Ngati ali ndi nthawi, mungakambirane naye mfundo zomwe zili pakamutu kakuti, “Mfundo Zinanso Zomwe Tikuphunzira M’Baibulo.”

  4. Perekani magaziniyo

  5. Konzani zoti mudzakumanenso ndi kukambirana funso lachiwiri

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena