MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Tingayambe Bwanji Kukambirana ndi Anthu Pogwiritsa Ntchito Timapepala?
Kungochokera mu January 2018, pachikuto cha Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu panayamba kupezeka zitsanzo za ulaliki. Kwa nthawi imeneyi, takhala tikulimbikitsidwa kumagwiritsa ntchito Baibulo m’malo momangogawira mabuku athu. Pofuna kuthandiza ofalitsa, panayamba kutuluka mavidiyo a zitsanzo za ulaliki zosonyeza mmene tingalalikirire ndi Baibulo lokha. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitiyeneranso kugawira mabuku athu tikamalalikira kunyumba ndi nyumba? Ayi. Tikutero chifukwa kugawira timapepala ndi njira yosavuta yoyambira kukambirana ndi anthu. Tikhoza kuyamba kukambirana ndi munthu pogwiritsa ntchito timapepala potsatira mfundo zotsatirazi:
Funsani funso lomwe lili patsamba loyamba la kapepalako.
Musonyezeni yankho la m’Baibulo pogwiritsa ntchito lemba (kapena malemba) lomwe lili patsamba lachiwiri. Ngati nthawi ilipo, werengani ndi kukambirana mfundo zomwe zili m’kapepalako.
Perekani kapepalako kwa mwininyumba ndipo mulimbikitseni kuti akawerenge.
Musanachoke, musonyezeni funso lomwe lili pamene alemba kuti “Ganizirani Mfundo Iyi” kenako muuzeni kuti mudzabweranso kuti mudzamusonyeze yankho la funsolo kuchokera m’Baibulo.
Mukadzapitanso, mudzakambirane naye yankho la funso munasiya lija ndipo mudzasiyenso funso loti mudzakambirane ulendo wotsatira. Mukhoza kupeza funso limeneli pawebusaiti yathu kapena m’buku lomwe lasonyezedwa patsamba lomaliza la kapepalako. M’kupita kwa nthawi mungamusonyeze kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu kapena chilichonse cha Zinthu Zophunzitsira.