CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 3-5
Mavuto Omwe Anabwera Chifukwa cha Bodza Loyamba
Satana wakhala akusocheretsa anthu kungochokera pamene ananamiza Hava. (Chiv. 12:9) Kodi mabodza a Satana otsatirawa amalepheretsa bwanji anthu kukhala pa ubwenzi ndi Yehova?
Kunja kuno kulibe Mulungu
Pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi
Mulungu alibe dzina
Mulungu amawotcha anthu ku Gehena kwamuyaya
Chilichonse chimene chimachitika ndi chifuniro cha Mulungu
Mulungu alibe nafe ntchito
Kodi mumamva bwanji mukamva mabodza amenewa?
Nanga mungathandize bwanji kuyeretsa dzina la Mulungu?