Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 January tsamba 8
  • Kodi Tingayambe Bwanji Kukambirana ndi Anthu Pogwiritsa Ntchito Timapepala?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingayambe Bwanji Kukambirana ndi Anthu Pogwiritsa Ntchito Timapepala?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Timapepala Tatsopano Anatikonza Bwino Kwambiri
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Zimene Tinganene
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Muzigwiritsa Ntchito Timapepala Pofalitsa Uthenga Wabwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 January tsamba 8
Mlongo akulalikira mwamwayi kwa mayi wina pasiteji ya basi pogwiritsa ntchito kapepala kakuti ‘Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingayambe Bwanji Kukambirana ndi Anthu Pogwiritsa Ntchito Timapepala?

Kungochokera mu January 2018, pachikuto cha Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu panayamba kupezeka zitsanzo za ulaliki. Kwa nthawi imeneyi, takhala tikulimbikitsidwa kumagwiritsa ntchito Baibulo m’malo momangogawira mabuku athu. Pofuna kuthandiza ofalitsa, panayamba kutuluka mavidiyo a zitsanzo za ulaliki zosonyeza mmene tingalalikirire ndi Baibulo lokha. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitiyeneranso kugawira mabuku athu tikamalalikira kunyumba ndi nyumba? Ayi. Tikutero chifukwa kugawira timapepala ndi njira yosavuta yoyambira kukambirana ndi anthu. Tikhoza kuyamba kukambirana ndi munthu pogwiritsa ntchito timapepala potsatira mfundo zotsatirazi:

  1. Funsani funso lomwe lili patsamba loyamba la kapepalako.

  2. Musonyezeni yankho la m’Baibulo pogwiritsa ntchito lemba (kapena malemba) lomwe lili patsamba lachiwiri. Ngati nthawi ilipo, werengani ndi kukambirana mfundo zomwe zili m’kapepalako.

  3. Perekani kapepalako kwa mwininyumba ndipo mulimbikitseni kuti akawerenge.

  4. Musanachoke, musonyezeni funso lomwe lili pamene alemba kuti “Ganizirani Mfundo Iyi” kenako muuzeni kuti mudzabweranso kuti mudzamusonyeze yankho la funsolo kuchokera m’Baibulo.

Kapepala kakuti ‘Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?’ kosonyeza mbali 4 zakapepalaka.

Mukadzapitanso, mudzakambirane naye yankho la funso munasiya lija ndipo mudzasiyenso funso loti mudzakambirane ulendo wotsatira. Mukhoza kupeza funso limeneli pawebusaiti yathu kapena m’buku lomwe lasonyezedwa patsamba lomaliza la kapepalako. M’kupita kwa nthawi mungamusonyeze kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu kapena chilichonse cha Zinthu Zophunzitsira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena