Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 June tsamba 8
  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Zimene Tinganene

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Zimene Tinganene
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Zimene Tinganene
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Kodi Tingayambe Bwanji Kukambirana ndi Anthu Pogwiritsa Ntchito Timapepala?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Zimene Tinganene
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 June tsamba 8

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Zimene Tinganene

Kuyambira mu January 2018, patsamba loyamba la Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, pakhala pakuikidwa zitsanzo za zimene tinganene. Kodi tingazigwiritse ntchito bwanji?

Mlongo akupanga chitsanzo pamsonkhano wa mkati mwa mlungu.

Mukamakamba Nkhani za Ophunzira: Muzigwiritsa ntchito funso, lemba, komanso funso la ulendo wotsatira zomwe zili m’chitsanzo cha zimene tinganene. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti muzinena ndendende zimene zili mu vidiyo ya zimene tinganene. Mukhoza kupanga chitsanzo chanu m’njira yosiyana ndi imene yagwiritsidwa ntchito m’vidiyo. Mungagwiritsenso ntchito mawu oyamba komanso kufotokoza mfundo za m’nkhani yanu mosiyana ndi zimene zili m’vidiyo. Mukhozanso kugawira buku kapena magazini opezeka mu Zinthu Zophunzitsira ngakhale kuti sizinatchulidwe m’malangizo a nkhani yanu.

Mlongo yemwe uja akulalikira mzimayi ndipo akumuwerengera lemba.

Mukakhala mu Utumiki: Cholinga cha zitsanzo za zimene tinganene ndi kutithandiza kudziwa mfundo zina zomwe tikhoza kufotokoza mu utumiki. Ngati munthu atasonyeza kuti akufuna kudziwa zambiri, mukhoza kupitiriza kukambirana naye, mwina pogwiritsa ntchito mfundo za m’chitsanzo cha ulendo wobwereza. Mukhoza kusintha chitsanzocho kapena kugwiritsa ntchito chitsanzo china chosiyana ndi chimenecho. Kodi nkhani imene munkagwiritsa ntchito mwezi watha kapena lemba lina losiyana ndi limene mukugwiritsa ntchito panopa, zikhoza kukopa kwambiri chidwi cha anthu a m’dera lanu? Kodi anthu a m’dera limene mumakhala amachita chidwi ndi nkhani komanso zinthu zomwe zangochitika kumene m’deralo? Ngakhale kuti mukhoza kugwiritsa ntchito zitsanzo za zimene tinganene m’njira zosiyanasiyana, cholinga chanu chizikhala kuchita ‘zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti muugawirenso kwa ena.’​—1 Akor. 9:22, 23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena