Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 July tsamba 16
  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Zimene Tinganene

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Zimene Tinganene
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Zimene Tinganene
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Kodi Tingayambe Bwanji Kukambirana ndi Anthu Pogwiritsa Ntchito Timapepala?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kukonza Ulaliki Wanuwanu wa Magazini
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 July tsamba 16
Zithunzi: 1. Mlongo ali ndi mwamuna wake ndipo akukambirana ndi mayi wina kunyumba kwake pogwiritsa ntchito kabuku kakuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka kalekale.” 2. Mlongo yemwe uja akupanga chitsanzo pa misonkhano ya mkati mwa wiki pogwiritsa ntchito kabuku kakuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka kalekale.”

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Zimene Tinganene

Abale amagwira ntchito mwakhama kwambiri kuti akonze zitsanzo za zimene tinganene ndipo ofalitsa ambiri amaona kuti zimawathandiza akakhala mu utumiki m’gawo lawo. Koma popeza kuti zinthu zimasiyanasiyana m’mayiko, ofalitsa ali ndi ufulu wogwiritsa ntchito njira ina kapena nkhani ina imene ingakope chidwi cha anthu a m’gawo lawo akakhala mu utumiki. Komabe, zimenezi sizikukhudza ntchito yapadera yolalikira, ndipo abale ndi alongo kulikonse ayenera kutsatira malangizo onse okhudza ntchitoyi. Cholinga chathu ndi kukwaniritsa zimene Yesu anatiuza zoti tilalikire uthenga wabwino wa Ufumu.​—Mt 24:14.

Ofalitsa akamakamba nkhani za ophunzira, azigwiritsa ntchito nkhani zimene zili mu zitsanzo za zimene tinganene zomwe zili mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu. Komabe, ngati asonyeza kuti akhoza kusintha mafunso, lemba, kapena zimene zikuchitika mu vidiyo kuti zigwirizane ndi mmene zinthu zilili m’deralo, akhoza kutero. Zimenezi zikusintha malangizo amene anali mu ndandanda ya utumiki wa June 2020 patsamba 8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena