Muzigwiritsa Ntchito Timapepala Pofalitsa Uthenga Wabwino
1. Kodi anthu a Mulungu akhala akugwiritsa ntchito bwanji timapepala?
1 Kwa nthawi yaitali, anthu a Yehova akhala akugwiritsa ntchito timapepala tofotokoza nkhani za m’Baibulo pofalitsa uthenga wabwino. Kuyambira m’chaka cha 1880, M’bale C. T. Russell ndi anzake anayamba kutulutsa timapepala timene abale ankagwiritsa ntchito pa nthawiyo polalikira. Timapepalati tinali tofunika kwambiri moti m’chaka cha 1884, pamene M’bale C. T. Russell ankalembetsa ku boma bungwe loyendetsa ntchito yolalikira za Ufumu, dzina lachingelezi la kapepala lakuti “tract” linalipo pa dzina lonse la bungwelo. Pa nthawiyo bungwelo linkadziwika kuti Zion’s Watch Tower Tract Society ndipo masiku ano limadziwika kuti Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Pofika m’chaka cha 1918, Ophunzira Baibulo, dzina limene tinkadziwika nalo pa nthawiyo, anali atafalitsa timapepala toposa 300 miliyoni. Timapepalati tikupitirizabe kuthandiza kwambiri pa ntchito yolalikira.
2. N’chifukwa chiyani timapepala tili tothandiza?
2 N’chifukwa Chiyani Tili Tothandiza?: Timapepala timakhala tokongola komanso tokopa chidwi. Uthenga wake umakhala wachidule komanso wosavuta kumva. Eninyumba amene sangafune kuwerenga magazini kapena buku sangavutike kuwerenga kapepala. Ngakhale ofalitsa atsopano komanso ana savutika kugawira timapepalati. Komanso, timapepalati timakhala tating’ono moti sitivuta kunyamula.
3. Fotokozani nkhani imene inakuchitikirani kapena imene inafalitsidwa m’mabuku athu yofotokoza kufunika kwa timapepala.
3 Anthu ambiri amaphunzira choonadi akawerenga kapepala. Mwachitsanzo, mayi wina wa ku Haiti anaona kapepala kathu mumsewu. Atatola kapepalako n’kukawerenga anafuula kuti, “Ndapeza choonadi!” Kenako anapita ku Nyumba ya Ufumu ndipo anayamba kuphunzira Baibulo, moti patapita nthawi anabatizidwa. Zimenezi zinachitika chifukwa cha mphamvu ya Mawu a Mulungu yopezeka pakapepala.
4. Kodi cholinga chathu chizikhala chiyani mwezi umene tikugawira timapepala?
4 Polalikira Kunyumba ndi Nyumba: Popeza timapepala ndi tothandiza, kuyambira mwezi wa November tizigwiritsa ntchito timapepalati nthawi ndi nthawi polalikira. Cholinga chathu chisamangokhala kugawira timapepalati, koma chizikhalanso chogwiritsa ntchito timapepalati poyamba kukambirana ndi anthuwo. Ngati mwininyumba atasonyeza chidwi pa ulendo woyamba kapena wobwereza, tingamusonyeze mmene timachitira phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena buku lina lililonse lophunzirira. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji timapepala polalikira kunyumba ndi nyumba? Popeza tili ndi timapepala tosiyanasiyana, tiyenera kudziwa bwino kapepala kamene tikugawira.
5. Kodi tingagawire bwanji timapepala polalikira kunyumba ndi nyumba?
5 Ulaliki wathu uzikhala wogwirizana ndi gawo komanso kapepala kamene tikugawira. Tingayambe kukambirana ndi mwininyumba mwa kumupatsa kapepala. Munthuyo angakopeke ndi chithunzi chimene chili patsamba loyamba la kapepalako. Kapena tingasonyeze mwininyumbayo timapepala tingapo n’kumulola kuti asankhe kamene kamusangalatsa. Tikamalalikira m’gawo limene anthu amachita mantha kutsegula zitseko, tikhoza kugwira kapepalako m’njira yoti mwininyumbayo aone zimene zili patsamba loyamba. Tikhoza kumupemphanso kuti tikalowetse pansi pa chitseko n’kumuuza kuti tikufuna timve maganizo ake. Ngati mutu wa kapepalako ndi funso, tingamupemphe kuti atiyankhe. Kapena tikhoza kumufunsa funso limene lingamuchititse chidwi kuti tiyambe kukambirana naye. Ndiyeno tikhoza kuwerenga ndime ina pakapepalako ndi mwininyimbayo, n’kumaima pamene pali funso kuti afotokoze maganizo ake. Tingawerenge m’Baibulo malemba amene akugwirizana kwambiri ndi mutu umene tikukambiranawo. Pambuyo pokambirana zina mwa mfundo zopezeka m’kapepalako, tingagwirizane naye zodzabweranso. Ngati ofalitsa m’gawolo amasiya mabuku pakhomo limene sanapeze anthu, tikhoza kusiya kapepalako pamalo amene anthu odutsa sangakaone.
6. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji timapepala polalikira mumsewu?
6 Polalikira Mumsewu: Kodi munagwiritsapo ntchito timapepala polalikira mumsewu? Nthawi zina timagwiritsa ntchito timapepala chifukwa anthu ena amene timakumana nawo amakhala akufulumira ndipo sapeza nthawi yoima kuti tikambirane nawo. Choncho zingakhale zovuta kudziwa ngati ali ndi chidwi kapena ayi. M’malo mongowapatsa magazini atsopano pamene sitikudziwa kuti akawerenga kapena ayi, bwanji osawapatsa kapepala? Popeza tsamba loyamba la kapepalako limakhala lokopa chidwi komanso uthenga wake umakhala wachidule, anthu akhoza kukopeka kuti awerenge kapepalako ngakhale pamene ali ndi nthawi yochepa. Koma ngati sakufulumira, tikhoza kukambirana nawo nkhani zina zimene zili pakapepalako.
7. Fotokozani zimene anthu ena amachita pogwiritsa ntchito timapepala polalikira mwamwayi.
7 Polalikira Mwamwayi: Timapepala sitivuta kugwiritsa ntchito polalikira mwamwayi. M’bale wina amaika timapepala m’thumba la malaya ake akamachoka pakhomo. Akakumana ndi munthu, monga wogwira ntchito m’sitolo, amamupempha kuti amupatse kapepala koti awerenge. Chitsanzo china ndi cha mwamuna wina ndi mkazi wake amene ankapita kumzinda wa New York City kuti akaone malo. Iwo anazindikira kuti akakumana ndi anthu ochokera kumayiko ena, choncho anatenga kabuku ka mutu wakuti, Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse ndiponso timapepala ta zilankhulo zosiyanasiyana. Ndiyeno ankati akapeza anthu olankhula chinenero cha kudziko lina, akugulitsa zinthu m’mbali mwa msewu, atakhala pansi kupaki kapena mulesitilanti, ankawagawira timapepala ta m’chinenero chawo.
8. Kodi timapepala timafanana bwanji ndi mbewu?
8 Fesani Mbewu Zanu: Tingayerekezere timapepala ndi mbewu. Mlimi amafesa mbewu mongomwaza chifukwa sadziwa zimene zingamere ndiponso kukula. Lemba la Mlaliki 11:6 limati: “[Fesa] mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo, chifukwa sukudziwa pamene padzachite bwino, kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzachite bwino.” Choncho, tiyeni tipitirize ‘kufalitsa zimene tikudziwa’ pogwiritsa ntchito timapepalati tomwe n’tothandiza kwambiri.—Miy. 15:7.
[Bokosi patsamba 3]
Popeza timapepala ndi tothandiza, kuyambira mwezi wa November tizigwiritsa ntchito timapepalati nthawi ndi nthawi polalikira.