Timapepala Tatsopano Anatikonza Bwino Kwambiri
1. Kodi ndi timapepala titi tomwe anatikonza bwino kwambiri?
1 Pa msonkhano wachigawo wa 2013 wakuti, ‘Mawu a Mulungu Ndi Choonadi’ panatuluka timapepala tokwana 5. Patapita nthawi, panatulukanso kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 38 kakuti, “Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?” Timapepala 6 tonseti anatikonza bwino kwambiri. Kodi n’chifukwa chiyani anatikonza chonchi? Nanga tingagwiritse ntchito bwanji timapepalati tikamalalikira kunyumba ndi nyumba?
2. Kodi n’chifukwa chiyani anapanga timapepala tosiyana ndi takale tija?
2 N’chifukwa Chiyani Anatikonza Choncho? Kuti tilalikire mogwira mtima kunyumba ndi nyumba timafunika kuchita zinthu 4 zotsatirazi: (1) Kufunsa munthu funso n’cholinga choti tiyambe kukambirana naye. (2) Kuwerenga lemba. (3) Kumupatsa kanthu koti awerenge. (4) Kumufunsa funso loti tidzakambirane pa ulendo wotsatira. Timapepala tatsopanoti timathandiza kuti tizitha kuchita zinthu 4 zimenezi mosavuta.
3. Kodi tingagawire bwanji timapepala tatsopanoti tikakhala mu utumiki?
3 Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Timapepalati? (1) Mukapereka moni, musonyezeni munthuyo funso lomwe lili patsamba loyamba la kapepala komanso mayankho atatu omwe ali pamenepo n’kumufunsa maganizo ake. (2) Musonyezeni mkati mwa kapepala pamene palembedwa mawu akuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa.” Ngati n’zotheka, werengani naye lemba lomwe lili pamenepo kuchokera m’Baibulo. Ngati ali ndi nthawi kambiranani naye pakamutu kakuti, “Kodi Zimenezi Zikutanthauza Chiyani?” (3) Mugawireni kapepalako n’kumulimbikitsa kuti akawerenge akatsala. (4) Musanapite, musonyezeni funso lomwe lili pansi pa mawu akuti, “Ganizirani Mfundo Iyi” ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane yankho la m’Baibulo la funsolo.
4. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji timapepala tatsopano pa ulendo wobwereza?
4 Kugwiritsa ntchito timapepalati pa ulendo wobwereza n’kosavutanso. Gwiritsani ntchito malemba amene ali patsamba lomaliza la kapepala poyankha funso lomwe munamufunsa pa ulendo woyamba. Musanapite, mulozereni chithunzi cha kabuku kakuti, Uthenga Wabwino. Musonyezeni kabukuka komanso phunziro logwirizana ndi nkhani ya m’kapepalako. Mufunseni ngati angafune kuti mumusiire kabukuko. Ngati wavomera, konzani zoti mudzaphunzire mutu umenewu pa ulendo wotsatira. Pamenepo ndiye kuti mwayambitsa phunziro. Kapenanso m’malo momusonyeza kabuku, mungamupatse kapepala kena n’kukonza zoti mudzakambirane za kapepalako pa ulendo wotsatira.
5. Kodi timapepala timatithandiza bwanji mu utumiki?
5 Takhala tikugwiritsa ntchito timapepala mu utumiki kwa zaka zoposa 130. Ngakhale kuti kukula komanso kaonekedwe ka timapepala kakhala kakusintha, timapepalati n’tothandizabe mu utumiki. Tiyeni tizigwiritsa ntchito timapepala tokonzedwa bwinoti kuti tipitirize kuthandiza anthu padziko lonse kudziwa choonadi cha m’Baibulo.—Miy. 15:7a.