Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Oct. 1
“Akatswiri ambiri amaona kuti bambo ali ndi udindo wofunika kwambiri m’banja. Kodi inu mukuganiza kuti munthu angatani kuti akhale bambo wabwino? [Yembekezani ayankhe.] Yesu ananena kuti chitsanzo cha Atate wake chinamuthandiza kwambiri. [Werengani Yohane 5:19.] Nkhani iyi ikufotokoza zinthu 6 zimene bambo ayenera kuchitira ana ake.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 18.
Galamukani Oct.
“Anthu a zipembedzo zosiyanasiyana sagwirizana chimodzi pofotokoza za mmene Mulungu alili. Koma kodi Mwana wa Mulungu anati chiyani pofotokoza za Mulungu? Taonani zimene Yesu ananena pa Yohane 4:24. [Werengani.] Nkhaniyi ikupereka yankho lomveka bwino la m’Baibulo, la funso lakuti, ‘Kodi Mulungu ndi wotani kwenikweni?’” M’sonyezeni nkhani imene ili pa tsamba 24 ndi 25.
Nsanja ya Olonda Nov. 1
“Anthu ambiri zimawavuta kumvetsa kuti Mulungu ndi wachikondi akaganizira chiphunzitso chakuti Iye amazunza anthu kosatha. Kodi inu maganizo anu ndi otani pankhani imeneyi? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu sachita zinthu mwankhanza. [Werengani Ezekieli 18:23.] Musangalala kwambiri ndi mfundo za m’Malemba zimene zafotokozedwa m’magazini iyi.”
Galamukani Nov.
“Anthu ambiri amaganiza kuti munthu amasangalala kwambiri akakhala wotchuka, wolemera, kapena akakhala ndi udindo wapamwamba. Kodi inuyo mumaonera chiyani kuti mudziwe kuti munthu akusangalala? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena kuti zingathandize munthu kukhala wosangalala. [Werengani Salmo 1:1-3.] Nkhani iyi ikufotokoza mfundo 6 zimene zingathandize kuti munthu akhale wosangalala.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 6.