N’zotheka Inuyo Kukhala Mphunzitsi
1. Kodi wofalitsa Ufumu aliyense ali ndi mwayi wochita chiyani?
1 Chimodzi mwa zinthu zosangalatsa kwambiri muutumiki ndicho kuphunzitsa munthu choonadi. Munthuyo akamalabadira uthenga wa Ufumu ndiponso tikamamuthandiza kuyandikira Wolamulira wa chilengedwe chonse, zimakhala zinthu zosaiwalika. (Yak. 4:8) Wofalitsa Ufumu aliyense afunika kukhala ndi cholinga chophunzitsa munthu amene ali ndi njala ya choonadi, ndi kuona kuti munthuyo akuyamba kusintha kwambiri umunthu wake, maganizo ndi khalidwe lake.—Mat. 28:19, 20.
2. N’chifukwa chiyani ena amalephera kuchititsa phunziro la Baibulo, nanga n’chiyani chingawathandize kuthetsa vutolo?
2 Dalirani Yehova: Nthawi zakale, atumiki okhulupirika ankakayikira ngati angakwanitse kuchita ntchito imene anapatsidwa. Koma kudalira Yehova Mulungu kunathandiza Mose, Yeremiya, Amosi ndi anthu ena, kuti asiye kuda nkhawa kapena kudzikayikira n’kuchita ntchito yaikulu yofunika. (Eks. 4:10-12; Yer. 1:6, 7; Amosi 7:14, 15) Nayenso mtumwi Paulo anafunika ‘kulimba mtima.’ Kodi chinamuthandiza ndi chiyani? Iye ananena kuti analimba mtima chifukwa cha “Mulungu wathu.” (1 Ates. 2:2) Inde, tonsefe tiyenera kudalira Yehova kutipatsa thandizo, nzeru ndi mphamvu zimene timafunikira pochititsa maphunziro a Baibulo opita patsogolo.—Yes. 41:10; 1 Akor. 1:26, 27; 1 Pet. 4:11.
3, 4. Kodi ndi zinthu zotani zimene zingatithandize pophunzitsa Mawu a Mulungu?
3 Khalani ndi Mtima Wofuna Kuphunzira: Mlangizi wathu wamkulu Yehova Mulungu, amatiphunzitsa nthawi zonse kudzera m’mapulogalamu auzimu kuti tikhale aphunzitsi oyenera mokwanira. (Yes. 54:13; 2 Tim. 3:16, 17) Sonyezani kuti muli ndi mtima wofuna kuphunzira mwa kuchita zonse zimene mungathe kuti muwadziwe bwino Malemba ndiponso kuti muwonjezere luso lanu lophunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Chimenechi ndicho cholinga chachikulu cha Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Msonkhano wa Utumiki. Komabe, misonkhano yonse ya mpingo imatiphunzitsa mmene tingagwiritsire ntchito Mawu a Mulungu pophunzitsa.
4 Yesetsani kuphunzira njira zosavuta zimene mungathe kuphunzitsira mfundo zozama za choonadi. Buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 227, limati: “Muyenera kuimvetsa bwino nkhani yanu inumwini kotero kuti mukaimveketse bwino kwa ena.” Komanso kuyankha pamisonkhano kumatithandiza kusaiwala mfundo zazikulu zimene tingadzazigwiritse ntchito m’tsogolo. Chotero, muzikonzekera bwino ndipo mukamatero, mudzasiya kudzikayikira komanso luso lanu lophunzitsa lidzawonjezereka.
5. Kodi mumpingo, tili ndi njira zinanso ziti zomwe zingatithandize kukhala aphunzitsi opita patsogolo?
5 Kuyambira kale, atumiki achikhristu akhala akuphunzira kwa anzawo pogwirira limodzi ntchito yopanga ophunzira. (Luka 10:1) Ngati ndi zotheka, mungapite kukachititsa maphunziro a Baibulo limodzi ndi ofalitsa aluso, kuphatikizapo apainiya, akulu, ndi oyang’anira oyendayenda. Onani mmene iwo amagwiritsira ntchito mafanizo osavuta ndi zinthu zina zimene mabuku athu amagwiritsa ntchito pofotokoza mfundo za m’Malemba. Afunseni zimene mungachite kuti mukhale mphunzitsi wabwino. (Miy. 1:5; 27:17) Zonsezi ndi njira zimene Mulungu amatiphunzitsira ndipo tifunika kuyamikira.—2 Akor. 3:5.
6. Kodi chofunika ndi chiyani kwenikweni kuti mukhale mphunzitsi wa Mawu a Mulungu?
6 Dalirani Yehova kuti mupindule ndi maphunziro amene iye akupereka. Muzipemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni kupita patsogolo. (Sal. 25:4, 5) Inunso mungasangalale chifukwa chothandiza munthu wina kukhala mphunzitsi wa Mawu a Mulungu ngati inuyo.