Yehova Akutiphunzitsa Kuti Tigwire Ntchitoyi
1. Yehova akamapatsa anthu ntchito yoti agwire, kodi amachitanso chiyani?
1 Yehova akamapatsa anthu ntchito yoti agwire, amaperekanso malangizo a mmene angagwirire ntchitoyo. Mwachitsanzo, Yehova atauza Nowa kuti amange chingalawa, ntchito imene Nowayo anali asanagwirepo, anamuuzanso mmene agwirire ntchitoyo. (Gen. 6:14-16) Pamene Mose, yemwe anali m’busa komanso munthu wofatsa, anatumidwa kukakumana ndi akuluakulu a Isiraeli ndi Farao, Yehova anamutsimikizira kuti: “Ine ndidzakhala nawe polankhula ndipo ndidzakuuza zonena.” (Eks. 4:12) N’chimodzimodzinso ndi ntchito yathu yolalikira. Yehova watipatsanso malangizo. Iye akutiphunzitsa mmene tingagwirire ntchito imeneyi kudzera mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndiponso Msonkhano wa Utumiki. Kodi tingatani kuti tizipindula ndi maphunziro amenewa?
2. Kodi tingapindule bwanji ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu?
2 Sukulu ya Utumiki wa Mulungu: Muzikonzekera nkhani zimene zili pandandanda musanapite kumsonkhano wa mpingo uliwonse. Mukamachita zimenezi, muzimvetsa bwino kwambiri ophunzira akamakamba nkhani zawo ndipo mudzakhala ndi luso lophunzitsa ena. (Miy. 27:17) Nthawi zonse muzitenga buku lanu la Sukulu ya Utumiki mukamapita kumsonkhano wa mpingo ndipo muziligwiritsa ntchito. Wochititsa sukulu akatchula bukuli, pamene wophunzira aliyense wamaliza nkhani yake, muzitseka mzere kunsi kwa mfundo zazikulu zimene mukufuna kuzigwiritsa ntchito ndipo muzilemba mfundo zina padanga limene lili m’mbali mwa bukuli. Njira yabwino kwambiri yopindulira ndi sukuluyi ndi kutenga nawo mbali. Kodi munalembetsa m’sukulu? Mukapatsidwa nkhani m’sukulu, muzikonzekera bwino ndiponso kutsatira malangizo amene mwapatsidwa. Mukakhala mu utumiki, muzigwiritsa ntchito zimene mwaphunzira.
3. Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tizipindula ndi Msonkhano wa Utumiki?
3 Msonkhano wa Utumiki: Kuti tizikumbukira mfundo zimene timamva pa msonkhano umenewu, tiziwerengeratu nkhani zimene tikakambirane ndiponso kukonzekera kuyankha. Tikamapereka ndemanga zazifupi ndiye kuti anthu ambiri aziperekanso ndemanga. Muzikhala tcheru kwambiri ena akamachita zitsanzo ndipo muzigwiritsa ntchito mfundo zimene mukuona kuti zingakuthandizeni kulalikira mogwira mtima mu utumiki. Muzisunga nkhani za mu Utumiki Wathu wa Ufumu zimene mungazigwiritse ntchito mu utumiki kuti mudzazigwiritsenso ntchito m’tsogolo.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira malangizo amene timalandira pa misonkhano?
4 Ntchito imene tapatsidwa, yolalikira uthenga wabwino padziko lonse lapansi, ndi yovuta ngati mmene inalilinso ntchito imene Nowa ndi Mose anauzidwa kuti achite. (Mat. 24:14) Tikhoza kugwira ntchitoyi bwinobwino ngati titadalira Yehova, Mlangizi Wamkulu, ndiponso kutsatira zimene akutiphunzitsa.—Yes. 30:20.