Kulalikira Kumatilimbitsa Mwauzimu
1. Kodi ntchito yolalikira ingatithandize bwanji?
1 Kugwira nawo ntchito yolalikira nthawi zonse kungalimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova komanso kungawonjezere chimwemwe chathu. N’zoona kuti cholinga chachikulu cha utumiki wathu ndi kusangalatsa Yehova. Komabe, chifukwa chomvera lamulo lakuti “lalika mawu,” timadalitsidwa ndi Yehova komanso timapindula m’njira zina. (2 Tim. 4:2; Yes. 48:17, 18) Koma kodi zingatheke bwanji kusangalala komanso kulimbikitsidwa chifukwa cholalikira?
2. Kodi kulalikira kumatilimbikitsa motani?
2 Timalimbikitsidwa Ndiponso Kudalitsidwa: Ntchito yolalikira imatithandiza kuganizira kwambiri za madalitso a Ufumu m’malo moganizira za mavuto athu. (2 Akor. 4:18) Tikamafotokozera anthu zimene Baibulo limaphunzitsa, chikhulupiriro chathu pa malonjezo a Yehova chimalimba ndiponso timayamikira kwambiri choonadi. (Yes. 65:13, 14) Tikamathandiza ena kukonda Yehova kuti ‘asakhale mbali ya dziko,’ nafenso timayesetsa kukhala osiyana ndi dziko. (Yoh. 17:14, 16; Aroma 12:2).
3. Kodi ntchito yolalikira imatithandiza bwanji kukhala ndi makhalidwe abwino?
3 Kugwira nawo ntchito yolalikira kumatithandiza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, tikamayesetsa kukhala “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana,” timakhala anthu odzichepetsa kwambiri. (1 Akor. 9:19-23) Kulalikira anthu “okalikakalika ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa,” kumatithandiza kukhala achisoni komanso oganizira ena. (Mat. 9:36) Timaphunzira kupirira tikamapitiriza kulalikira ngakhale tikumane ndi anthu opanda chidwi kapena otsutsa. Timakhala ndi chimwemwe chochuluka tikamagwiritsa ntchito nthawi yathu kuthandiza ena.—Mac. 20:35.
4. Kodi mumamva bwanji ndi utumiki wanu?
4 Ndi mwayi waukulu kuchita utumiki umene umatamanda Mulungu, yemwe ndi woyenera kumulambira. Utumikiwu umatilimbikitsa ndiponso umabweretsa madalitso ambiri kwa aliyense amene ‘amachitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino’ ndi mtima wonse.—Mac. 20:24.