Phunzitsani Anthu Amene Amavutika Kuwerenga
1. Kodi tingakumane ndi vuto lotani tikamalalikira?
1 Tikamalalikira, nthawi zina timakumana ndi anthu amene amavutika kuwerenga. Kodi tingawathandize bwanji?
2. N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza anthu amene amavutika kuwerenga, ndipo tingachite bwanji zimenezi?
2 Muziwalemekeza: Yehova amaona mtima wa munthu osati maphunziro ake. (1 Sam. 16:7; Miy. 21:2) Choncho, si bwino kunyoza anthu amene amavutika kuwerenga. Anthu otere angayamikire kwambiri thandizo lathu ngati tikuwalemekeza ndiponso kuleza nawo mtima. (1 Pet. 3:15) Njira imodzi yochitira zimenezi ndi kusawakakamiza kuti awerenge lemba kapena ndime. Munthu akamaphunzira choonadi chapamwamba chopezeka m’Baibulo, amachita khama kuti akulitse luso lake lowerenga. Amatero kuti azisangalala chifukwa chowerenga Mawu a Mulungu ndi ‘kulingirira [kusinkhasinkha, NW] usana ndi usiku.’—Sal. 1:2, 3.
3. Kodi tingagwiritse ntchito njira ziti pophunzitsa anthu amene amavutika kuwerenga?
3 Njira Zophunzitsira Anthu Baibulo: Kugwiritsa ntchito zithunzi ndi njira yabwino yophunzitsira, chifukwa imathandiza wophunzira kukumbukira zimene waphunzira. Mungafunse wophunzirayo zimene akuona pachithunzi chimene chili m’buku limene mukuphunzira. Kenako mungamufunse mafunso amene angamuthandize kumvetsa zimene akuphunzira pachithunzicho. Gwiritsani ntchito malemba amene akuphunzitsa mfundo inayake imene ili pachithunzicho. Mungagwiritsenso ntchito zithunzi pobwereza mfundo zimene mwaphunzira. Pewani kuphunzitsa zinthu zambirimbiri nthawi imodzi. Tsindikani mfundo yaikulu ya nkhaniyo ndi mfundo zina zofunika, ndipo pewani kufotokoza zinthu zimene sizili m’nkhani imene mukuphunzirayo. Werengani malemba kuchokera m’Baibulo, ndipo mufunseni wophunzirayo kuti afotokoze ngati wamvetsa lembalo. Zimenezi zingam’thandize kufuna kukulitsa luso lake lowerenga, n’cholinga choti azitha kufufuza choonadi cha m’Baibulo payekha.
4. Kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kuyamba kuwerenga bwino?
4 Zinthu Zothandiza Kuwerenga Bwino: Anthu amene amavutika kuwerenga kapena amene analibe mwayi wopita kusukulu, angathe kumvetsa bwino zimene aphunzitsidwa. Mungawalimbikitse kutsatira m’buku lawo pamene akumvetsera CD kapena DVD, mwinanso angamatchule mawu amene akumvetserawo chamumtima. Zimenezi zingawathandize kuti ayambe kuwerenga bwino. Mwinanso kabuku kakuti Dziperekeni pa Kuwerenga ndi Kulemba kangawathandize. M’madera ena, akulu amakonza zoti pampingo pakhale kalasi yophunzitsa kuwerenga. Pogwiritsa ntchito njira zimenezi, tingathandize anthu amene amavutika kuwerenga kuti amvetse “malemba opatulika,” amene angawathandize kukhala ndi nzeru kuti adzapulumuke.—2 Tim. 3:15.