‘Perekani Moyo Wanu’ kwa Ophunzira Anu
1. Kodi chimafunika n’chiyani kuti tithandize wophunzira Baibulo?
1 Kuti tithandize ophunzira Baibulo mpaka kufika podzipereka kwa Mulungu, pamafunika zambiri osati kungochititsa phunziro la Baibulo lokhazikika basi. Mtumwi Paulo anayerekezera chikondi chimene anali nacho pa anthu amene ankawaphunzitsa ndi chikondi chimene mayi woyamwitsa amakhala nacho pa mwana wake. Ifenso timasangalala kupereka ‘moyo wathu’ n’cholinga choti tithandize anthu amene timawaphunzitsa Baibulo kukula mwauzimu.—1 Ates. 2:7-9.
2. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza chikondi kwa anthu amene timaphunzira nawo, ndipo kodi tingachite bwanji zimenezi?
2 Muziwasonyeza Chikondi: Wophunzira Baibulo akayamba kutsatira zimene akuphunzira, chikumbumtima chake chimamuletsa kupitiriza kucheza ndi anthu amene zochita zawo sizigwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. (1 Pet. 4:4) Ndiponso abale ake angayambe kudana naye. (Mat. 10:34-36) Kuti asamakhumudwe, tiyenera kumusonyeza chikondi. M’bale wina yemwe wagwira ntchito ya umishonale kwa zaka zambiri anati: “Si bwino kufulumira kuchoka mukangomaliza kuphunzira naye. Ngati n’kotheka, muzicheza kaye pang’ono.” Muziona zinthu zimene wophunzira wanuyo akufunikira, n’kumuthandiza. Mwachitsanzo, mungamuimbire foni kapena kukamuona akadwala. Mungachitenso bwino kukhala naye pafupi kumisonkhano komanso kumuthandiza kusamalira ana, ngati pangafunike kutero.
3. Kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kuti azilimbikitsidwa ndi mpingo?
3 Mpingo Ungathadize: Ngati mukulalikira pafupi ndi nyumba ya wophunzira wanuyo, mungachite bwino kukamuona mwachidule kuti adziwane ndi m’bale kapena mlongo amene mukuyenda naye mu utumiki. Ngati n’zotheka, popita kukachititsa phunziro muzitenga ofalitsa osiyanasiyana, kuphatikizapo akulu. Komanso mukangoyamba kuphunzira ndi munthu Baibulo, ndi bwino kumulimbikitsa kuti azipezeka pa misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Zimenezi zingamuthandize kuti adziwane komanso kulimbikitsidwa ndi anthu mumpingo omwe angadzakhale abale ake auzimu.—Maliko 10:29, 30; Aheb. 10:24, 25.
4. Kodi tingapeze phindu lotani tikamathandiza mwakhama anthu amene timaphunzira nawo Baibulo?
4 Makolo amene satopa kuphunzitsa ana awo zinthu zauzimu, amasangalala kwambiri anawo akayamba kutumikira Yehova ndi kuyenda m’choonadi. (3 Yoh. 4) Ifenso tingasangalale ngati timapereka moyo wathu pothandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo.