Mfundo Zitatu Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muziphunzitsa Mogwira Mtima
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tiziphunzitsa anthu mogwira mtima?
1 Ofalitsa tonse ndife aphunzitsi. Kaya tikulankhula koyamba ndi munthu, kupitanso kwa munthu kuti tikakulitse chidwi chake kapena kuchititsa phunziro la Baibulo, timakhala tikuphunzitsa basi. Zimene timaphunzitsa anthu ndi zinthu zofunika kwambiri. Timawathandiza kumvetsa “malemba oyera” amene angawapatse ‘nzeru zowathandiza kuti adzapulumuke.’ (2 Tim. 3:15) Kodi kugwira ntchito imeneyi si mwayi waukulu? Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene zingatithandize kuti tiziphunzitsa anthu mogwira mtima.
2. Kodi tingatani kuti tiziphunzitsa zinthu zosavuta kumva?
2 Zosavuta kumva: Tikamvetsetsa nkhani ina yake, tikhoza kuiwala kuti munthu amene sakuidziwa nkhaniyo angavutike kuti aimvetse. Choncho, mukamachititsa phunziro la Baibulo, musamanene mfundo zambiri zosafunikira. Muzifotokoza mfundo zikuluzikulu zokha. Kudziwa kuphunzitsa sikutanthauza kulankhula zinthu zambirimbiri ayi. (Miy. 10:19) Komanso ndi bwino kuwerenga malemba okhawo amene ali ofunikadi pa nkhaniyo. Mukawerenga lemba, muzingofotokoza mawu a palembapo amene akukhudzana kwambiri ndi nkhani imene mukukambiranayo basi. Pa ulaliki wa paphiri umene umapezeka pa Mateyu chaputala 5 mpaka 7, Yesu anaphunzitsa mfundo zikuluzikulu za choonadi. Koma ananena mfundozo pogwiritsa ntchito mawu ochepa ndiponso osavuta kumva.
3. Kodi mafanizo ndi zithunzi zili ndi phindu lotani, ndipo ndi mafanizo otani amene amakhala abwino kwambiri?
3 Mafanizo ndi zithunzi: Mafanizo ndi zithunzi zimathandiza anthu kuganiza, kukhudzidwa ndi nkhaniyo ndiponso kukumbukira zimene mwakambirana. Sizidalira kuti munthu akhale wodziwa kufotokoza bwino nkhani kuti azinena mafanizo abwino. Yesu ankanena mafanizo aafupi komanso osavuta kumva. (Mat. 7:3-5; 18:2-4) Mukhozanso kujambula zithunzi zosavuta papepala kuti muthandize munthu kumvetsa mfundo inayake. Zimenezi zimathandiza kwambiri. Mukamakonzekera bwino mukhoza kumapeza mafanizo ogwira mtima.
4. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mafunso pothandiza wophunzira kuti amvetse zimene akuphunzira?
4 Mafunso: Wophunzira amafunika kuganiza kaye asanayankhe funso limene mwam’funsa. Choncho muzileza mtima poyembekezera kuti ayankhe funso. Mukayankha nokha funsolo poona kuti iye akuchedwa kuyankha, simungadziwe ngati wophunzirayo wamvetsadi mfundoyo. Ngati wayankha molakwika, ndi bwino kumufunsa mafunso ena amene angamuthandize kuyankha molondola m’malo moyankha inuyo funsolo. (Mat. 17:24-27) Palibe munthu amene ndi mphunzitsi wangwiro. Choncho, Baibulo limatilimbikitsa kuti nthawi zonse tizisamala ndi zimene timaphunzitsa. Tikatero, ifeyo ndiponso anthu amene amatimvetsera, tidzapeza madalitso osatha.—1 Tim. 4:16.