Sangalalani Chifukwa Choti Mwagwira Ntchito Mwakhama
1. Kodi n’chiyani chimene chingachepetse khama lathu pa utumiki?
1 Anthufe tinalengedwa m’njira yakuti ‘tikagwira ntchito mwakhama, tizisangalala.’ (Mlal. 2:24) Komabe tikaona kuti utumiki wathu ulibe zotsatira zabwino, tingayambe kugwa ulesi ndipo zimenezi zingapangitse kuti tikhale osasangalala komanso khama lathu lingachepe. Kodi tingatani kuti tizikhalabe osangalala ndi utumiki?
2. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyembekezera zinthu zimene sizingachitike pa utumiki wathu?
2 Musamayembekezere Zinthu Zoti Sizingachitike: Tiyenera kukumbukira kuti ngakhale kuti ndi anthu ochepa okha amene anakhala otsatira a Yesu, utumiki wake unali wopindulitsa. (Yoh. 17:4) M’fanizo lake lonena za wofesa mbewu, Yesu ananeneratu kuti anthu ambiri sadzalandira uthenga wa Ufumu womwe uli ngati mbewu. (Mat. 13:3-8, 18-22) Ngakhale zili choncho, khama lathu limathandiza anthu ambiri.
3. Kodi timabereka bwanji zipatso ngakhale titapanda kuona zotsatira zambiri za utumiki wathu?
3 Mmene Timabalira Zipatso Zochuluka: Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena m’fanizo lija, anthu amene amalandira uthenga wabwino ‘amabala zipatso.’ (Mat. 13:23) Mmera wachimanga ukakula n’kukhwima, umabereka chimanga osati mmera wina wachimanga ayi. Izi zikutanthauza kuti zipatso zimene Akhristu amabala si anthu atsopano amene amalowa m’choonadi ayi, koma mbewu zambiri za Ufumu, kapena kuti kulalikira kwambiri za Ufumu. Zotsatira zake n’zakuti timakhala okhutira ngakhale anthu atapanda kuphunzira choonadi. Izi zili choncho chifukwa timakhalabe titathandizira kuyeretsa dzina la Yehova. (Yes. 43:10-12; Mat. 6:9) Timasangalalanso chifukwa chakuti ndife antchito anzake a Mulungu. (1 Akor. 3:9) Ndipotu “chipatso cha milomo” yathu chimenechi chimasangalatsa Yehova.—Aheb. 13:15, 16.
4. Kodi utumiki wathu ungakhale ndi zotsatira zotani zimene sitingathe kuzidziwa?
4 Kuwonjezera pamenepa, khama lathu pa ntchitoyi likhoza kukhala ndi zotsatira zimene sitingazione. N’kutheka kuti anthu ena amene anamva ulaliki wa Yesu anakhala otsatira ake pambuyo poti Yesuyo wamaliza utumiki wake wa padziko lapansi. Mofanana ndi zimenezi, mbewu za Ufumu zimene timafesa sizingamere komanso kukula mumtima mwa munthu nthawi yomweyo. Koma mwina m’tsogolo akhoza kudzayamba choonadi ifeyo osadziwa. Zimenezi zikusonyeza kuti utumiki wathu umakhala ndi zotsatira zabwino kwambiri. Chotero tiyeni ‘tipitirize kubala zipatso zambiri’ ndi kusonyeza kuti ndifedi ophunzira a Yesu.—Yoh. 15:8.