Webusaiti Yathu Yovomerezeka Yakonzedwa Kuti Izithandiza Ifeyo Komanso Anthu Ena
Yesu anatilamula kuti tilalikire uthenga wabwino wa Ufumu “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Pofuna kutithandiza ‘kukwaniritsa mbali zonse za utumiki wathu,’ mawebusaiti atatu omwe ndi www.watchtower.org, www.jw-media.org ndi www.jw.org, aphatikizidwa n’kukhala Webusaiti imodzi ya jw.org yomwe yakonzedwanso.—2 Tim. 4:5.
“Padziko Lonse Lapansi Kumene Kuli Anthu:” Anthu ambiri padziko lapansi amagwiritsa ntchito Intaneti. Anthu ambiri, makamaka achinyamata, akugwiritsa ntchito Intaneti pofuna kudziwa zinthu zosiyanasiyana. Webusaiti yathu ikuthandiza anthu amene amagwiritsa ntchito Intaneti kupeza mayankho olondola a mafunso a m’Baibulo. Webusaitiyi imathandizanso anthu kudziwa nkhani zokhudza gulu la Yehova. Pa Webusaitiyi afotokozaponso mosavuta zimene munthu angachite kuti apemphe munthu woti aziphunzira naye Baibulo panyumba kwaulere. Chotero, Webusaitiyi ikuthandiza kuti uthenga wabwino ufike m’madera osiyanasiyana padziko lapansili, amene anthu ake alibe mwayi wochuluka womva uthenga wa Ufumu.
“Mitundu Yonse:” Kuti “mitundu yonse” ya anthu imve choonadi cha m’Baibulo, uthengawu uyenera kulalikidwa m’zinenero zosiyanasiyana. Anthu amene azifika pa Webusaiti ya www.jw.org azitha kupeza nkhani m’zinenero mahandiredi ambirimbiri, kuposa Webusaiti iliyonse.
Igwiritseni Ntchito: Webusaiti ya www.jw.org yomwe yakonzedwanso, sikuti ndi yothandiza anthu omwe si a Mboni okha ayi. Yakonzedwanso n’cholinga choti ifeyo tiziigwiritsa ntchito. Ngati mumagwiritsa ntchito Intaneti, tikukulimbikitsani kuti muidziwe bwino Webusaiti ya www.jw.org. M’munsimu muli malangizo a mmene mungagwiritsirire ntchito Webusaitiyi.
[Chithunzi patsamba 3]
(Onani mu Utumiki wa Ufumu kuti mumvetse izi)
Iyeseni
1 Lembani www.jw.org pamalo olembapo adiresi pa Intaneti.
2 Fufuzani zimene mukufuna pa Webusaitiyi potsegula pamene pali mitu ya nkhani imene ili pamwamba, timitu ta nkhani tomwe tili m’mbali, komanso pamene pali mawu ena omwe akusonyeza mzere kunsi kwake mukafikapo.
3 Gwiritsani ntchito Webusaiti ya www.jw.org pa zipangizo za m’manja zomwe zili ndi Intaneti, monga mafoni. Tsamba la nkhani lakonzedwa kuti lizitha kukwana pazipangizo zazing’ono, monga pafoni, koma uthenga wake uzikhala wofanana.