Muzigwiritsa Ntchito Webusaiti Yathu mu Utumiki—“Kuyankha Mafunso a M’Baibulo”
Mbali ina yomwe imapezeka pa webusaiti yathu ya jw.org/ny yakuti, “Zimene Baibulo Limaphunzitsa,” ili ndi nkhani za mutu wakuti, “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo.” Nkhanizi zimayankha mafunso amene anthu amakonda kufunsa. Kudziwa bwino nkhani zimenezi kungatithandize kuti tiziuza anthu kuti apite pa webusaiti yathu n’kupeza mayankho a m’Baibulo pogwiritsa ntchito nkhanizi. Tingagwiritsenso ntchito nkhanizi poyamba kukambirana ndi anthu. Tingasankhe funso limene anthu ambiri a m’dera lathu angachite nalo chidwi. Kenako tingafunse munthu maganizo ake. Ndiyeno tingamuuze yankho la m’Baibulo la funsolo pogwiritsa ntchito mfundo zomwe zili m’nkhani imene ili pa webusaiti yathu. Tikatero tingamusonyeze kapena kumufotokozera mmene angapezere nkhaniyo pa webusaiti yathu. Njira ina, tingafunse munthu funso, kutsegula webusaiti yathu n’kumupempha kuti awerenge yankho la funsolo pa webusaitiyi. Mkazi wa woyang’anira dera wina amakonda kuyamba ndi mawu akuti: “Anthu ambiri amadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika?’ Kodi mungakonde kudziwa yankho la funso limeneli kwa masekondi 51 okha?” Kenako amatsegula foni kapena chipangizo chomwe ali nacho kuti munthuyo amvetsere yankho la funsolo limene anapanga dawunilodi. Pomaliza amamusonyeza mutu 11 m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.