Muzigwiritsa Ntchito Webusaiti Yathu mu Utumiki—“Khalani Bwenzi la Yehova”
Pa webusaiti yathu ya jw.org/ny pagawo lakuti, “Zimene Baibulo Limaphunzitsa” pali mbali yakuti “Khalani Bwenzi la Yehova.” Pa mbaliyi pali nyimbo, mavidiyo komanso zoti ana achite. Kodi munayamba mwagwiritsa ntchito mbali imeneyi polalikira? Ngati mukuphunzira Baibulo ndi munthu amene ali ndi ana, mungathe kumusonyeza mbaliyi. Zimenezi zingachititse kuti akhale ndi chidwi choonanso zinthu zina zomwe zili pawebusaiti yathuyi.
Pa nthawi imene tinkagawira Uthenga wa Ufumu Na. 38, m’bale wina anagawira kapepalaka kwa mayi wina ndipo mayiyo anayamba kukawerenga nthawi yomweyo. Mayiyu ali ndi ana angapo ndipo anawo anayamba kuchita chidwi ndi kapepalako. M’baleyo ataona zimenezi anafotokozera mayiyo mwachidule zomwe zili m’kapepalako n’kumulozera adiresi ya webusaiti yathu yomwe ili patsamba lomaliza la kapepalako. Mayiyu atasangalala kwambiri ndi zimenezi, m’baleyo anagwiritsa ntchito foni yake n’kumusonyeza iyeyo ndi ana ake vidiyo imodzi ya Kalebe.
Mlongo wina anauza mnzake wakuntchito yemwe ali ndi ana za webusaiti yathu komanso nkhani zokhudza mabanja zomwe zili pa webusaitiyi. Mayiyu atapita kunyumba, anatsegula webusaitiyi ali limodzi ndi ana ake. Atakumananso ndi mlongo uja anamuuza kuti ana ake anasangalala kwambiri ndi webusaitiyi moti ankazungulirazungulira akuimba nyimbo yakuti, “Lalikira Mawu.” Anawa anamva nyimboyo muvidiyo yakuti, “Khalani Bwenzi la Yehova.”
Tikukulimbikitsani kuti inunso muone zinthu zosiyanasiyana zomwe zili pa webusaiti yathu. Mungathenso kupanga dawunilodi vidiyo, nyimbo kapena zoti ana achite n’kukhala nazo pa foni yanu kapena chipangizo china kuti muzisonyeza anthu mukamalalikira. Mbali yakuti, “Khalani Bwenzi la Yehova” ingatithandize kwambiri kuti tizitumikira Yehova monga akapolo.—Mac. 20:19.