Polalikira, Muzigwiritsa Ntchito Webusaiti Yathu Yovomerezeka
Limbikitsani Anthu Kuti Azigwiritsa Ntchito Webusaitiyi: Anthu ena amene amazengereza kuti tilankhule nawo kapena kuti alandire mabuku athu, angavomere kufufuza okha nkhani zokhudza Mboni za Yehova pa www.jw.org kunyumba zawo. Choncho muziuza anthu za Webusaitiyi nthawi iliyonse, ngati kuchita zimenezo kuli kotheka.
Kuyankha Mafunso: Nthawi zina mwininyumba, munthu wachidwi kapena munthu amene timadziwana naye angafunse funso lokhudza Mboni za Yehova kapena zikhulupiriro zathu. Zikatero muzimusonyeza yankho la funsolo nthawi yomweyo popita pa Webusaitiyi pafoni kapena pakompyuta. Nthawi zambiri zimakhala bwino kuwerenga mwachindunji kuchokera m’Baibulo malemba amene asonyezedwa pa nkhani yomwe ili pa Webusaitiyi. Ngati pa nthawiyo mulibe foni kapena kompyuta imene mungagwiritse ntchito Intaneti, fotokozerani munthuyo mmene angagwiritsire ntchito www.jw.org kuti apeze yekha yankho la funso lakelo.—Pitani pa Webusaiti ya jw.org, kenako pitani pamutu wakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa/Kuyankha Mafunso a m’Baibulo, kapena Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova/Mafunso Amene Anthu Amafunsa Kawirikawiri.”
Tumizani Nkhani Kapena Buku: Tumizani nkhani ya pa PDF kapena EPUB imene mwaikopera pa Webusaitiyi ku imelo ya munthu wachidwi. Kapena koperani nkhani yongomvetsera pa CD. Nthawi iliyonse imene mwatumizira munthu wosabatizidwa buku, kabuku kapena magazini athunthu osati mbali chabe, muziwerengera monga zinthu zimene mwagawira mwezi umenewo.—Pitani pamutu wakuti “Mabuku Ndiponso Zinthu Zina.”
Onetsani Munthu Nkhani Zimene Zangochitika Kumene Zokhudza Mboni za Yehova: Zimenezi zidzathandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo komanso anthu amene mukuwalalikira kuchita chidwi ndi ntchito yathu ya padziko lonse komanso mgwirizano wathu. (Sal. 133:1)—Pitani pamutu wakuti “Nkhani.”
[Chithunzi patsamba 5]
(Onani mu Utumiki wa Ufumu kuti mumvetse izi)
Iyeseni
1Pitani pamutu wakuti “Mabuku ndi Zinthu Zina.” Kenako pezani buku limene mukufuna kukopera, kenako sindikizani batani kuti mupeze nkhani yowerenga kapena yomvetsera imene mukufuna.
2 Pitani pamene alemba kuti MP3 kuti muone ndandanda ya nkhani zosiyanasiyana. Pitani pamutu wa nkhani kuti muikopere kapena ▸ kuti muimvetsere.
3 Sankhani chinenero pamndandanda wa zinenero ngati mukufuna kukopera buku la chinenero chakunja.