Gwiritsani Ntchito Webusaiti Yathu Yovomerezeka Pothandiza Munthu Wolankhula Chinenero China
Muonetseni Webusaiti Yathu: Musonyezeni mmene angagwiritsire ntchito mndandanda wa zinenero kuti alowe pa Webusaitiyi m’chinenero chake. (M’zinenero zina, Webusaitiyi ikupezeka mbali zochepa zokha.)
Muonetseni Tsamba la Webusaitiyi M’chinenero Chake: Tsegulani tsamba la buku lathu, monga la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena kapepala kakuti Kudziwa Choonadi. Kenako sankhani chinenero cha mwininyumbayo pamndandanda wa zinenero.
Mutsegulireni Nkhani Yoti Amvetsere: Pezani nkhani yomvetsera imene ili m’chinenero cha munthuyo kenako itseguleni kuti amvetsere.—Pitani pamutu wakuti “Mabuku ndi Zinthu Zina/Mabuku ndi Timabuku,” kapena “Mabuku ndi Zinthu Zina/Magazini.”
Lalikirani Ogontha: Ngati mutapeza munthu wogontha, muonetseni vidiyo ya m’chinenero chamanja ya chaputala cha m’Baibulo, buku, kabuku kapena kapepala.—Pitani pamutu wakuti “Mabuku ndi Zinthu Zina/Chinenero Chamanja.”
[Chithunzi patsamba 6]
(Onani mu Utumiki wa Ufumu kuti mumvetse izi)
Iyeseni
1 Tsegulani apa ▸ kuti muonere vidiyo imene mwasankha kapena pitani pamene alemba kuti “Koperani” kuti mukopere.
2 Sankhani chinenero china pamndandanda wa zinenero kuti tsamba limene mukufunalo likhale m’chinenerocho.
3 Pitani pamene alemba kuti “Tsamba Lotsatira” kapena “Za M’katimu” kuti muwerenge nkhani kapena mutu wina.