Zimene Mungachite Ngati Mukufuna Mabuku Achinenero China Mwamsanga
Nthawi zina timakumana ndi anthu ena omwe amakonda kuwerenga mabuku a m’chinenero china amene sitimakhala nawo kumpingo. Kodi mumadziwa kuti ngati muli ndi Intaneti komanso makina osindikizira mabuku, mukhoza kusindikiza nokha mabuku a m’zinenero pafupifupi 400? Mungachite zimenezi motere:
• Pa kompyuta yanuyo pitani pa adiresi iyi: www.jw.org/ny.
• Kumanja kwa tsamba lomwe mwatsegulalo, kuli mndandanda wa zina mwa zinenero zosiyanasiyana zimene mabuku athu akupezekamo. Tabwanyani pa kachithunzi ka dziko kuti muone mndandanda wa zinenero zonse.
• Tabwanyani pa chinenero chimene mukufuna. Tsamba lidzatseguka losonyeza zinthu zimene mukhoza kusindikiza, monga timapepala, timabuku, ndiponso nkhani zina. Popeza kuti tsamba limeneli limakhala m’chinenero chomwe mwasankhacho, musade nkhawa ngati simukutha kuzindikira mitu ya mabukuwo.
• Tabwanyani buku lililonse limene mukufuna. Mukatero nkhani za m’bukulo zidzaonekera pa kompyutapo, ndipo mukhoza kuzisindikiza pogwiritsa ntchito kachizindikiro kosindikizira kamene kali pa kompyutayo.
Adiresi yathu ya pa Intaneti imeneyi, imangokhala ndi zinthu zochepa, choncho mukafuna mabuku owonjezera mukhoza kuitanitsa kudzera kumpingo. Mukaona kuti munthuyo ali ndi chidwi, ndi bwino kuitanitsa mabuku kudzera kumpingo.