Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/13 tsamba 2
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Mlongo Ayenera Kuvala Chinachake Kumutu pa Zochitika Ziti, Ndipo N’chifukwa Chiyani?
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Chititsani Maphunziro a Baibulo Achidule Ndiponso a Patelefoni Opita Patsogolo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo Achidule Pakhomo ndi pa Telefoni
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 11/13 tsamba 2

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi mlongo ayenera kuvala chinachake kumutu akapita limodzi ndi m’bale ku phunziro lake la Baibulo lachidule limene limachitika ataimirira pakhomo la munthu?

Mlongo akamachititsa phunziro la Baibulo la nthawi zonse m’bale ali pompo, ayenera kuvala chinachake kumutu. (1 Akor. 11:3-10) Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002, tsamba 27 inanena kuti, ‘kumeneku n’kuphunzitsa ndipo mlongoyo amakhala atakonzekera kuti akukaphunzitsa. Pamenepa amakhala akutsogolera ndithu ndipo phunziro lotereli ndi mbali ya maphunziro a mpingo. Ngati mlongo akuchititsa phunziro loterolo pali m’bale, ayenera kuvala chinachake kumutu.’ Zimenezi zingachitike kaya phunzirolo ndi la nthawi zonse, lachidule limene amachita ataimirira kapena phunziro lililonse.

Koma ngati phunziro la Baibulo lachidule limene timachita titaimirira silinakhazikitsidwe bwinobwino, mlongo sayenera kuvala chinachake kumutu akapita ndi m’bale. Angachite zimenezi ngakhale zitakhala kuti cholinga chawo ndi kukasonyeza mmene timachitira phunziro kapena kukambirana nkhani inayake yochokera m’buku kapena kabuku kamene timaphunzitsira anthu. Popeza nthawi zambiri pamafunika kuchita maulendo obwereza angapo kuti phunziro loterolo likhazikike, mlongo ayenera kuganizira mmene zinthu zilili kuti adziwe nthawi yoyamba kuvala chinachake kumutu akapita limodzi ndi m’bale kuphunziroli.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena