1914-2014 Patha Zaka 100 Ufumu wa Mulungu Ukulamulira!
Mu 1922, M’bale J.F. Rutherford ananena kuti: “Onani, Mfumu yayamba kale kulamulira . . . Lengezani za Mfumu ndi ufumu wake.” Tsopano patha zaka 100 Ufumu wa Mulungu ukulamulira, ndipo mawuwa akupangitsa kuti nafenso masiku ano tizilengeza za Ufumuwu mosangalala. Tiyeni tiyesetse kuthandiza anthu kuti adziwe zokhudza Ufumu wa Mulungu kudzera pa webusaiti yathu. Zimenezi zipangitsa kuti mwezi wa August chaka chino ukhale wosaiwalika.