Patha Zaka 100 Tikulengeza za Ufumu
1. Kodi anthu a Yehova analimbikitsidwa kuchita chiyani zaka pafupifupi 100 zapitazo?
1 “Onani, Mfumu yayamba kale kulamulira ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza za ufumuwo. Choncho lengezani, lengezani, lengezani za Mfumu ndi ufumu wake.” M’bale Rutherford ndi amene analankhula mawu olimbikitsawa zaka pafupifupi 100 zapitazo. Anthu amene anamva mawu amenewa anayamba kulengeza uthenga wa Ufumu padziko lonse. Ifenso masiku ano timagwira ntchito yolengeza za Ufumu umenewu. Mofanana ndi Akhristu oyambirira, talalikira uthenga wabwino wa Ufumu “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Popeza tsopano patha zaka pafupifupi 100 tikulalikira za Ufumuwu, kodi takwanitsa kuchita zotani? Nanga kodi tingatani kuti tipitirizebe kulengeza za Ufumuwu?
2. Kodi magazini athu athandiza bwanji anthu kudziwa za Ufumu wa Mulungu?
2 Zimene Tachita pa Zaka Zimenezi: Kwa zaka zambiri tsopano, mabuku athu akhala akuthandiza anthu kudziwa za Ufumu wa Mulungu. Kuchokera mu 1939 magazini yathu yaikulu yakhala ikudziwika kuti, Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Nthawi zambiri m’magaziniyi mumakhala nkhani zonena za Ufumu wa Mulungu komanso zimene udzachite. Tilinso ndi magazini ya Galamukani! imene imatsindika mfundo yakuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto a anthu. M’pake kuti magazini awiriwa ndi amene amamasuliridwa m’zinenero zambiri komanso kufalitsidwa kwambiri padziko lonse kuposa magazini ena onse.—Chiv. 14:6.
3. Tchulani njira zimene tagwiritsa ntchito polengeza za Ufumu?
3 Anthu a Yehova akhala akugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana polengeza Ufumu wa Mulungu. Kale tinkagwiritsa ntchito mawailesi, magalamafoni ndi magalimoto okhala ndi zokuzira mawu. Njira zimenezi zinathandiza kuti tizilalikira uthenga wabwino pa nthawi imeneyi, pamene olengeza Ufumu anali ochepa. (Sal. 19:4) M’zaka za posachedwapa, tayamba kugwiritsa ntchito webusaiti yathu ya jw.org polengeza za Ufumu kwa anthu ambiri, kuphatikizapo amene ali m’mayiko omwe ntchito yathu ndi yoletsedwa.
4. Kodi pali njira zinanso ziti zimene tikugwiritsa ntchito polengeza za Ufumu?
4 Palinso njira zina zimene anthu a Yehova akhala akugwiritsa ntchito polengeza za Ufumu. Mwachitsanzo, kuchokera mu 1990, kuwonjezera pa kulalikira kunyumba ndi nyumba, tinayambanso kulalikira m’mapaki, m’malo oimika magalimoto komanso m’malo a malonda. Posachedwapa pakhazikitsidwanso njira yapadera yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri ndipo ntchito imeneyi ikuchitika m’mizinda ikuluikulu padziko lonse. Kuwonjezera pamenepa, mipingo ikumalalikiranso m’malo opezeka anthu ambiri amene ali m’gawo la mpingo wawo pogwiritsa ntchito njira yoika matebulo pamalo amene pamadutsa anthu ambiri. Komabe, kulalikira kunyumba ndi nyumba ndiye njira yaikulu imene tikugwiritsabe ntchito kulengeza za Ufumu wa Mulungu.—Mac. 20:20.
5. Kodi ambirife tikhala ndi mwayi wotani chaka chautumiki chikubwerachi?
5 Zimene Tikuyembekezera Kuchita Kutsogoloku: Tikuyembekezera kuti m’mwezi wa September, tikamayamba chaka chautumiki chatsopano, ofalitsa ambiri ayamba kuchita upainiya wokhazikika. Kodi nanunso mungakwanitse kukhala mpainiya wokhazikika? Ngati simungakwanitse, kodi mungathe kumachita upainiya wothandiza nthawi ndi nthawi? Ngakhale zitakhala kuti simungakwanitse kuchita upainiya, sitikukayikira kuti Yehova akudalitsani mukamayesetsa kuchita zambiri polalikira uthenga wa Ufumu.—Mal. 3:10.
6. N’chifukwa chiyani mwezi wa October chaka chino uli wapadera?
6 Pofika mwezi wa October 2014, Ufumu wa Mulungu ukhala utakwanitsa zaka 100 kuchokera pamene unakhazikitsidwa. M’pake kuti Nsanja ya Olonda yogawira ya October ili ndi nkhani zokhudza Ufumu wa Mulungu. Tikukulimbikitsani kuti mudzayesetse kugawira magaziniyi kwa anthu ambiri. Pamene tikuyembekezera zabwino kutsogoloku, tiyeni tonse tipitirizebe “kulengeza uthenga wabwino wonena za ufumu wa Mulungu” kwa onse amene angamvetsere.—Mac. 8:12.