Mwezi wa August Udzakhala Wosaiwalika
Tidzagawira Kapepala Katsopano Padziko Lonse
1. Kodi tidzagwira ntchito yapadera iti pamene kwangotsala pang’ono kuti Ufumu wa Mulungu ukwanitse zaka 100?
1 Posachedwapa Ufumu wa Mulungu ukwanitsa zaka 100 kuchokera pamene unakhazikitsidwa. Kodi sizingakhale bwino kuti tidzagwire ntchito yapadera posonyeza kuyamikira Yehova chifukwa cha zimenezi? M’mwezi wa August, tidzagawira padziko lonse kapepala katsopano kamutu wakuti, Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo? Kapepalaka kakulimbikitsa anthu kuti azifufuza m’Baibulo mayankho a mafunso amene angakhale nawo. Kakufotokozanso mmene webusaiti yathu ya jw.org/ny ingawathandizire.
2. Kodi tingatani kuti tidzagwire nawo ntchito yapadera yomwe idzachitike mu August?
2 Tidzatamanda Yehova: Pofuna kuthandiza aliyense amene akufuna kudzachita zambiri mu utumiki m’mwezi wa August, pakonzedwa zoti ofalitsa obatizidwa angathe kudzachita upainiya wothandiza wa maola 30. Popeza mweziwu udzakhala ndi masiku a Lachisanu, Loweruka ndi Lamlungu 5, ofalitsa amene amagwira ntchito kapena amene ali pa sukulu angathe kudzachita upainiya wothandiza. Ngati muli ndi wophunzira kapena mwana woti akhoza kupendedwa n’kukhala wofalitsa wosabatizidwa, dziwitsani wogwirizanitsa ntchito za m’bungwe la akulu mwachangu. Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri kugwira ntchito yapaderayi limodzi ndi ofalitsa atsopanowa. Nthawi zambiri apainiya okhazikika amapuma m’mwezi wa August chifukwa amakhala atakwanitsa maola ofunika pa chaka. Komabe angathe kusintha nthawi yawo yopumayo n’kudzapuma nthawi ina, n’cholinga choti adzagwire nawo ntchito yapaderayi mokwanira. Mabanja ayenera kuyamba kukonzekera panopa kuti adzathe kugwira nawo ntchitoyi, komwe kudzakhale ngati ‘kufuula mokweza kwambiri potamanda Yehova.’—Ezara 3:11; Miy. 15:22.
3. Kodi tikuyembekezera zotani pa ntchito yapaderayi?
3 M’mbuyomu takhala tikugwira ntchito yapadera yogawira zinthu zosiyanasiyana. Koma tikukhulupirira kuti ntchito imene tidzagwire m’mwezi wa August idzakhala yosaiwalika. Tikuyembekezera kuti m’mweziwu tidzakhala ndi chiwerengero chokwera cha maola, ofalitsa komanso apainiya othandiza kuposa m’mbuyo monsemu. Pamene chaka chautumiki cha 2014 chikupita kumapeto, tikupempha Yehova kuti adalitse zimene mtumiki wake aliyense adzachite m’mwezi wa August pogwira ntchito yapaderayi.—Mat. 24:14.