CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MIYAMBO 27-31
Baibulo Limafotokoza Zimene Mkazi Wabwino Amachita
M’chaputala 31 cha buku la Miyambo muli malangizo omwe Mfumu Lemueli inapatsidwa ndi mayi ake. Malangizowo anali omuthandiza kudziwa mmene angasankhire mkazi wabwino.
Mkazi wabwino amakhala wodalirika
Amakhala wogonjera komabe amafotokoza maganizo othandiza pamene banja likusankha zochita
Mwamuna wake amamudalira kuti akhoza kusankha yekha zinthu zina mwanzeru moti sayembekezera kuti azichita kumuuza zoyenera kuchita pa chilichonse
Mkazi wabwino amakhala wakhama ndiponso wanzeru
Amagwiritsa ntchito ndalama mwanzeru ndipo safuna zinthu zapamwamba. Amachita zimenezi n’cholinga choti banja lake lizioneka bwino ndiponso lizikhala ndi chakudya chokwanira
Amagwira ntchito mwakhama ndiponso kusamalira banja lake nthawi zonse
Mkazi wabwino amakonda Yehova
Amaopa Mulungu ndiponso amayesetsa kukhala naye pa ubwenzi wolimba