Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 November tsamba 2
  • “Mwamuna Wake Amadziwika Pazipata”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mwamuna Wake Amadziwika Pazipata”
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Uphungu Wanzeru wa Mayi
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Baibulo Limafotokoza Zimene Mkazi Wabwino Amachita
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Kusonyeza Chikondi ndi Ulemu Monga Mkazi
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kusonyeza Chikondi ndi Ulemu Monga Mwamuna
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 November tsamba 2

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Mwamuna Wake Amadziwika Pazipata”

Mkazi wabwino amathandiza kuti mwamuna wake azilemekezedwa ndi ena. Kale m’nthawi ya Mfumu Lemueli, mwamuna amene anali ndi mkazi wabwino ‘ankadziwika pazipata.’ (Miy. 31:23) Masiku ano amuna olemekezeka amatha kutumikira monga akulu kapena atumiki othandiza. Ngati ndi okwatira amakhala oyenerera kutumikira pa udindo mumpingo ngati akazi awo ali ndi makhalidwe abwino. (1 Tim. 3:4, 11) Akazi oterewa amayamikiridwa kwambiri ndi amuna awo komanso anthu onse mumpingo.

Mkazi akulankhula mwachikondi kwa mwamuna wake, akusamalira ana pamene mwamuna wake akuchita zinthu zokhudza mpingo komanso mkaziyo akugula chakudya

Mkazi wabwino amathandiza mwamuna wake kutumikira pa udindo . . .

  • pomulimbikitsa ndi mawu okoma mtima.—Miy. 31:26

  • polola kuti azigwiritsa ntchito nthawi ina kuti azithandiza anthu ena mumpingo.—1 Ates. 2:7, 8

  • pokhala ndi moyo wosalira zambiri.—1 Tim. 6:8

  • popewa kumufunsa nkhani zachinsinsi zokhudza mpingo.—1 Tim. 2:11, 12; 1 Pet. 4:15

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena