CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 25-28
Khalani Olimba Mtima Ngati Yeremiya
Yeremiya anachenjeza kuti Yerusalemu adzawonongedwa ngati mmene anawonongedwera Silo
Pa nthawi ina, likasa la pangano lomwe linali umboni woti Yehova ankatsogolera anthu ake, linkasungidwa ku Silo
Yehova analola kuti Afilisiti akalande likasalo ndipo silinabwererenso ku Silo
Ansembe, aneneri ndi anthu onse ankafuna kupha Yeremiya
Anthu anagwira Yeremiya chifukwa ankanena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi
Yeremiya sanathawe kapena kusiya kutumikira Mulungu
Yehova anateteza Yeremiya
Yeremiya anapitiriza kukhala wolimba mtima ndipo Yehova sanamusiye
Mulungu anachititsa kuti Ahikamu, yemwe anali wolimba mtima, ateteze Yeremiya
Yeremiya analengeza uthenga kwa zaka 40 ngakhale kuti anthu ambiri sankasangalala nawo. Iye anakwanitsa zimenezi chifukwa choti yehova ankamulimbikitsa komanso kumuthandiza