CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 12-13
Fanizo la Tirigu ndi Namsongole
Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la tirigu ndi namsongole posonyeza nthawi komanso zimene adzachite akamadzasankha Akhristu odzozedwa omwe ali ngati tirigu, zomwe zinayamba kuchitika mu 33 C.E.
‘Munthu anafesa mbewu zabwino m’munda wake’
Wofesa mbewu: Yesu Khristu
Mbewu zabwino zinafesedwa: Ophunzira a Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera
Munda: Anthu
“Anthu ali m’tulo, kunabwera mdani wake. Mdaniyo anafesa namsongole m’munda wa tiriguwo”
Mdani: Mdyerekezi
Anthu ali m’tulo: Atumwi onse atamwalira
“Zilekeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola”
Tirigu: Akhristu odzozedwa
Namsongole: Akhristu onyenga
“Choyamba sonkhanitsani namsongole . . . Mukatha mupite kukasonkhanitsa tirigu”
Akapolo kapena okolola: Angelo
Kusonkhanitsa namsongole: Akhristu onyenga akusiyanitsidwa ndi Akhristu odzozedwa
Kusonkhanitsa tirigu n’kukamuika munkhokwe: Akhristu odzozedwa akusonkhanitsidwa mumpingo wachikhristu
Pamene ntchito yokolola inkayamba, kodi n’chiyani chinasiyanitsa Akhristu oona ndi onyenga?
Kodi ndingapindule bwanji ngati nditamvetsa tanthauzo la fanizoli?