MOYO WATHU WACHIKHRISTU
KUWONJEZERA LUSO LATHU MU UTUMIKI—Muzigwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso
KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Ngati “maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya,” ndiye kuti mafunso ali ngati chotungira madziwo. (Miy. 20:5) Mafunso amathandiza kuti omvera afotokoze maganizo awo ndipo zingatithandize kudziwa mmene tingawathandizire. Yesu ankagwiritsa ntchito mafunso mwaluso. Ndiye kodi ifeyo tingamutsanzire bwanji?
KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?
Muzifunsa mafunso omwe angachititse munthu kufotokoza maganizo ake. Yesu ankakonda kufunsa mafunso amene ankachititsa ophunzira ake kufotokoza maganizo awo. (Mat. 16:13-16; be 238 ¶3-5) Kodi mungafunse mafunso ati kuti mudziwe maganizo a wophunzira wanu?
Muzifunsa mafunso othandiza munthu kupeza yekha yankho lolondola. Pofuna kuthandiza Petulo kukhala ndi maganizo oyenera, Yesu anamufunsa mafunso omuthandiza kupeza yankho lolondola. (Mat. 17:24-26) Kodi mungafunse mafunso ati pofuna kuthandiza wophunzira kuti apeze yekha yankho lolondola?
Muzimuyamikira wophunzira wanu. Mlembi wina ‘atayankha mwanzeru,’ Yesu anamuyamikira. (Maliko 12:34) Kodi mungayamikire bwanji wophunzira ngati wayankha funso limene mwafunsa?
ONERANI MBALI YOYAMBA YA VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRA NTCHITO IMENE YESU ANAGWIRA—MUZIPHUNZITSA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
N’chifukwa chiyani kumeneku sikuphunzitsa kwabwino ngakhale kuti mfundozo n’zolondola?
N’chifukwa chiyani kuphunzitsa kumafuna zambiri osati kungofotokoza mfundo?
ONERANI MBALI YACHIWIRI YA VIDIYOYI KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi m’baleyu wagwiritsa ntchito bwanji mafunso mwaluso?
Kodi ndi zinthu zina ziti zimene m’baleyu wachita zomwe tingatengere?
Kodi zimene timaphunzitsa zimakhudza bwanji anthu ena? (Luka 24:32)