Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 March tsamba 7
  • “Khalanibe Maso”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Khalanibe Maso”
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Fanizo la Anamwali Limatiphunzitsa Kufunika Kokhala Tcheru
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Anamwali Anzeru ndi Opusa
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Mumamvera Machenjezo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 March tsamba 7
Anamwali 10 a m’fanizo la Yesu

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 25

“Khalanibe Maso”

25:1-12

Ngakhale kuti fanizo la anamwali 10 limanena za otsatira odzozedwa a Khristu, mfundo zake zimakhudza Akhristu onse. (w15 3/15 12-16) Iye anati, “Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.” (Mat. 25:13) Kodi mungakwanitse kufotokoza bwinobwino fanizoli?

  • Mkwati (vesi 1)​—Yesu

  • Anamwali ochenjera omwe anakonzekera (vesi 2)​—Akhristu odzozedwa omwe ndi okonzeka kugwira ntchito yawo mokhulupirika ndipo adzawala ngati zounikira mpaka m’nthawi yamapeto. (Afil. 2:15)

  • Mawu ofuula akuti: “Mkwati uja wafika!” (vesi 6)​—Chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu

  • Anamwali opusa (vesi 8)​—Akhristu odzozedwa omwe anapita kukachingamira mkwati koma analephera kukhalabe maso ndipo analephera kukhalabe okhulupirika

  • Anamwali ochenjera anakana kugawana mafuta awo ndi anamwali opusa (vesi 9)​—Pambuyo poti Yehova wadinda chidindo chomaliza Akhristu odzozedwa, zidzakhala zosatheka kuti odzozedwa okhulupirikawa athandize osakhulupirika aja

  • “Mkwati anafika” (vesi 10)​—Yesu adzabwera kudzapereka chiweruzo chakumapeto kwa chisautso chachikulu

  • Anamwali ochenjera analowa limodzi ndi mkwati m’nyumba imene munali phwando laukwati, ndipo chitseko chinatsekedwa (vesi 10)​—Yesu adzasonkhanitsa odzozedwa okhulupirika n’kupita nawo kumwamba, koma osakhulupirika sadzalandira nawo mphoto imeneyi

Fanizoli silimasonyeza kuti Akhristu ambiri odzozedwa adzakhala osakhulupirika ndipo padzafunika kuti ena awalowe m’malo. M’malomwake, limangopereka chenjezo kwa Mkhristu aliyense wodzozedwa kuti akhoza kusankha yekha pakati pa kukhala wokonzeka komanso watcheru kapena kukhala wopusa ndiponso wosakhulupirika. Yesu anati, “Khalani okonzeka.” (Mat. 24:44) Kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena ayi, Yesu amafuna kuti tonse tikhale okonzeka kuti tichite utumiki wathu mokhulupirika komanso kukhalabe maso mpaka mapeto.

Kodi ineyo ndimasonyeza bwanji kuti ndili maso?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena