CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 27-28
Kodi Tingamvere Bwanji Lamulo Lakuti, Pitani Mukaphunzitse Anthu?
N’chifukwa chiyani tiyenera kulalikira? Yesu anapatsidwa ulamuliro waukulu ndi Yehova
Kodi tiyenera kukalalikira kuti? Yesu analamula otsatira ake kuti akaphunzitse “anthu a mitundu yonse”
Kuphunzitsa ena kuti azisunga zinthu zonse zimene Yesu analamula sikumatha
Kodi tingaphunzitse bwanji ena zimene Yesu analamula?
Kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kuti azigwiritsa ntchito zimene Yesu anaphunzitsa?
Kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kuti azitengera chitsanzo cha Yesu?