MOYO WATHU WACHIKHRISTU
N’chifukwa Chiyani Sitiyenera Kulowerera Ndale? (Mika 4:2)
Fanizo la Msamariya wachifundo limatithandiza kudziwa kuti Yehova ndi Mulungu wopanda tsankho. Iye amafuna kuti ‘tichitire onse zabwino’ kuphatikizapo anthu omwe timasiyana nawo maphunziro, mtundu, fuko kapena chipembedzo.—Agal. 6:10; Mac. 10:34.
ONERANI VIDIYO YAKUTI, N’CHIFUKWA CHIYANI SITIYENERA KULOWERERA NDALE? (MIKA 4:2), KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi timadziwa bwanji kuti lemba la Mika 4:2 limanena zimene zikuchitikira anthu a Mulungu masiku ano?
Kodi tingapewe bwanji ndale, nanga ubwino wake ndi wotani?
Kodi lemba la Chivumbulutso 13:16, 17, likusonyeza bwanji kuti andale amayesetsa kusokoneza maganizo komanso zochita zathu?
Kodi ndi zinthu zitatu ziti zomwe zingachititse kuti tiyambe kuchita nawo zandale kapena kukonda dziko lathu?