CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 20-21
“Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”
Asodzi aluso ankakhala oleza mtima, akhama komanso ankapirira mavuto osiyanasiyana n’cholinga choti aphe nsomba zambiri. (w12 8/1 18-20) Makhalidwe amenewa akanathandiza Petulo monga msodzi wa anthu. Komabe Petulo ankafunika kusankha chinthu choti aike pamalo oyamba m’moyo wake. Ankafunika kusankha ntchito yausodzi yomwe ankaikonda kwambiri kapena kudyetsa otsatira a Yesu mwauzimu.
Kodi mwasintha zinthu zotani pa moyo wanu kuti muziika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba?