CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 1-3
Mpingo Wachikhristu Unalandira Mzimu Woyera
Ayuda ambiri omwe anapita ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E. anali oti achokera m’mayiko ena. (Mac. 2:9-11) Ngakhale kuti ankatsatira Chilamulo cha Mose, Ayuda amenewa ayenera kuti anakhala m’mayiko omwe anachokerawo kwa moyo wawo wonse. (Yer. 44:1) Choncho n’kutheka kuti ambiri mwa anthuwa ankalankhula komanso kuoneka ngati anthu a m’mayikowo, osati ngati Ayuda. Pamene anthu 3,000 ochokera m’mayiko enawa anabatizidwa, mpingo wachikhristu unakhala ndi anthu a mitundu yosiyanasiyana. Ngakhale kuti anthuwa anali osiyana, “tsiku ndi tsiku anali kusonkhana kukachisi mogwirizana.”—Mac. 2:46.
Kodi mungasonyeze bwanji chidwi chenicheni kwa . . .
anthu a m’gawo lanu amene anachokera m’mayiko ena?
abale ndi alongo a mumpingo wanu omwe anachokera m’mayiko ena?