CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 1-3
Yehova ndi “Mulungu Amene Amatitonthoza M’njira Iliyonse”
Njira imodzi imene Yehova amagwiritsa ntchito potitonthoza ndi kugwiritsira ntchito abale ndi alongo athu mumpingo. Kodi tingalimbikitse bwanji Akhristu amene aferedwa?
Muziwamvetsera ndipo musamawadule mawu
“Lirani ndi anthu amene akulira.”—Aroma 12:15
Mungawalembere khadi, kalata, imelo kapena meseji yowalimbikitsa.—w17.07 15, bokosi
Mukhoza kupemphera nawo limodzi komanso kuwatchula m’mapemphero anu