Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 April tsamba 8
  • Dziperekeni Kuti Yehova Akuphunzitseni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziperekeni Kuti Yehova Akuphunzitseni
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Kodi Mungakonde Kufunsira Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Mukhale ndi Zolinga mu Chaka Chautumiki Chikubwerachi​—Funsirani Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Sukulu Yophunzitsa Utumiki—Khomo Lalikulu Loloŵera M’ntchito Yochuluka
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 April tsamba 8

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Dziperekeni Kuti Yehova Akuphunzitseni

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Yehova, yemwe ndi Mlangizi wathu wamkulu, amatipatsa maphunziro apamwamba kwambiri. Amatiphunzitsa kuti tisinthe moyo wathu komanso amatithandiza kuti tidzakhale ndi moyo wabwino m’tsogolo. Iye amachita zimenezi kwaulere. (Yes. 11:6-9; 30:20, 21; Chiv. 22:17) Pogwiritsa ntchito maphunziro amenewa, Yehova amatithandiza kuti tikhale okonzeka kuuza ena uthenga umene ungawathandize kuti adzapulumuke.​—2 Akor. 3:5.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Tiyenera kukhala odzichepetsa komanso ofatsa.​—Sal. 25:8, 9

  • Muzigwiritsa ntchito mwayi wamaphunziro umene muli nawo panopa, mwachitsanzo mukapatsidwa nkhani za ophunzira mumsonkhano wamkati mwa mlungu, muziyesetsa kuzikamba bwino

  • Khalani ndi zolinga zauzimu zomwe mungazikwaniritse.​—Afil. 3:13

  • Sinthani zinthu zina ndi zina kuti mupitirize kuphunzitsidwa ndi Yehova.​—Afilipi 3:8

ONERANI VIDIYO YAKUTI TINAPEZA MADALITSO AMBIRI CHIFUKWA CHOPHUNZITSIDWA NDI YEHOVA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ofalitsa ena alimbana ndi mavuto otani kuti akwanitse kulowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?

  • Kodi anthu amaphunzira zotani akalowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?

  • Kodi abale ndi alongo anathandiza bwanji Akhristu omwe anatumizidwa mumpingo wawo atamaliza maphunziro awo?

  • Kodi Mkhristu ayenera kukwaniritsa zinthu ziti kuti alowe nawo mu Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu? (kr 189)

  • Kodi ndi masukulu ena ati omwe mungalowe m’gulu la Yehova?

Abale ndi alongo omwe anamaliza maphunziro awo a Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu ku Namibia, Norway, United States ndi Japan

Kodi mungapeze madalitso otani ngati mutalola kuti Yehova akuphunzitseni?

MASUKULU A GULU LATHU OMWE NDINALOWAPO:

  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

  • Sukulu ya Utumiki Waupainiya

  • Sukulu ya Utumiki wa Ufumu

  • Sukulu ya Akulu

  • Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu

KODI NDI SUKULU ITI YA GULU LATHU YOMWE NDIKUFUNA KUDZALOWA?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena