Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 August tsamba 3
  • Muzicheza ndi Anthu Amene Amakonda Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzicheza ndi Anthu Amene Amakonda Yehova
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Yoasi Anasiya Kutumikira Yehova Chifukwa Chocheza ndi Anthu Ochita Zoipa
    Nsanja ya Olonda—2009
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Yehova?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Yehova Amadalitsa Anthu Amene Amachita Zinthu Molimba Mtima
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Yehoyada Anali Wolimba Mtima
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 August tsamba 3

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzicheza ndi Anthu Amene Amakonda Yehova

N’chifukwa chiyani tiyenera kumacheza ndi anthu amene amakonda Yehova? Chifukwa chake ndi choti anthu amene timacheza nawo angachititse kuti tikhale ndi makhalidwe abwino kapena oipa. (Miy. 13:20) Mwachitsanzo, Mfumu Yehoasi inkachita “zoyenera pamaso pa Yehova” chifukwa chokonda kucheza ndi Yehoyada yemwe anali mkulu wa ansembe. (2 Mbiri 24:2) Koma Yehoyada atangomwalira, Yehoasi anayamba kuchita zoipa chifukwa chocheza ndi anthu oipa.​—2 Mbiri 24:17-19.

M’nthawi ya atumwi, Paulo anayerekezera mpingo wachikhristu ndi ‘nyumba yaikulu’ ndipo anthu a mumpingo anawayerekezera ndi “ziwiya,” kapena kuti zipangizo zogwiritsa ntchito pakhomo. Timakhalabe “chiwiya cha ntchito yolemekezeka” tikamapewa kucheza ndi aliyense amene amachita zinthu zimene Yehova amadana nazo ngakhale atakhala wa m’banja lathu kapena wa mumpingo wathu. (2 Tim. 2:20, 21) Choncho, tiyeni tizicheza ndi anthu amene amakonda Yehova komanso amene amatilimbikitsa kuti tizimutumikira.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, MUZIPEWA KUGWIRIZANA NDI ANTHU A MAKHALIDWE OIPA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi tingayambe bwanji kucheza ndi anthu oipa?

  • N’chiyani chomwe chinathandiza Akhristu atatu m’vidiyoyi kuti asiye kugwirizana ndi anthu oipa?

  • Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingakuthandizeni kusankha mwanzeru anthu ocheza nawo?

John akupungulira vinyo alendo ake kulesitilanti; Kristin akuona zimene zili pamalo ochezera a pa intaneti; Jayden akusewera gemu pa intaneti; John ndi banja lake, Kristin komanso Jayden ali ku misonkhano

Kodi ndine “chiwiya cha ntchito yolemekezeka”?​—2 Tim. 2:21

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena