MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mumakonda Kwambiri Mawu a Mulungu?
Yehova Mulungu ndiye mwiniwake wa Baibulo. Choncho mfundo ndi mawu onse opezeka m’bukuli ndi zochokera kwa iyeyo. (2 Pet. 1:20, 21) Baibulo limasonyeza kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake posonyeza kuti iye ndiye woyenera kulamulira ndiponso kuti posachedwapa anthu onse adzakhala mosangalala. Baibulo limatithandizanso kudziwa makhalidwe ochititsa chidwi omwe Atate wathu wakumwamba ali nawo.—Sal. 86:15.
Anthu amakonda Mawu a Mulungu pazifukwa zosiyanasiyana. Koma tingasonyeze kuti Mawuwa ndi ofunika kwambiri pamoyo wathu, tikamawawerenga tsiku lililonse komanso tikamagwiritsa ntchito mfundo zake. Tiziyesetsa kuti zochita zathu zizigwirizana ndi zimene wolemba masalimo wina ananena kuti: “Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.”—Sal. 119:97.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ANKALEMEKEZA KWAMBIRI BAIBULO (WILLIAM TYNDALE), KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
N’chifukwa chiyani William Tyndale anamasulira mbali zina za Baibulo?
N’chifukwa chiyani tingati zimene anachita pomasulira Baibulo n’zochititsa chidwi?
Kodi Baibulo la Tyndale linkazembetsedwa bwanji polowa m’dziko la England?
Kodi aliyense angasonyeze bwanji kuti amakonda kwambiri Mawu a Mulungu?