CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 25-26
Esau Anagulitsa Ukulu Wake
Esau ‘sanayamikire zinthu zopatulika.’ (Ahe 12:16) Iye anagulitsa ukulu wake ndipo kenako anakwatira akazi awiri achikunja.—Ge 26:34, 35.
DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimayamikira zinthu zopatulika zotsatirazi?’
Ubwenzi wanga ndi Yehova
Mzimu woyera
Kudziwika ndi dzina loyera la Yehova
Ntchito yolalikira
Misonkhano
Ukwati