CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 8-9
Farao Yemwe Anali Wonyada Anathandiza Kukwaniritsa Cholinga cha Mulungu Mosadziwa
Mafumu a ku Iguputo ankadziona ngati milungu. Zimenezi zikutithandiza kumvetsa chifukwa chake Farao anali wonyada kwambiri moti sankafuna kumvera Mose ndi Aroni ngakhalenso ansembe ake ochita zamatsenga.
Kodi inuyo mumamvetsera anthu ena akamafotokoza maganizo awo? Kodi mumayamikira munthu wina akakupatsani uphungu? Kapena mumadziona kuti simulakwitsa? “Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko.” (Miy 16:18) Choncho tiyenera kupewa mtima wonyada.