CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 10-11
Mose ndi Aroni Anasonyeza Kulimba Mtima Kwambiri
Mose ndi Aroni anasonyeza kulimba mtima kwambiri pamene ankayankhula ndi Farao, yemwe pa nthawiyo anali mfumu yamphamvu kwambiri padziko lonse lapansi. Kodi n’chiyani chinawathandiza? Ponena za Mose, Baibulo limati: “Mwa chikhulupiriro anachoka mu Iguputo, koma osati chifukwa choopa mfumu ayi, pakuti anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Ahe 11:27) Mose ndi Aroni ankakhulupirira kwambiri Yehova ndipo ankamudalira.
Kodi ndi zochitika ziti zomwe zingafune kuti mulimbe mtima kuti mufotokoze zimene mumakhulupirira kwa munthu waudindo?