CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 15-16
Tamandani Yehova Poimba Nyimbo
Nyimbo zikhoza kukhudza kwambiri mmene timaganizira komanso mmene timamvera. Kuimba ndi kofunika kwambiri polambira Yehova.
Mose ndi Aisiraeli anaimba nyimbo zotamanda Yehova pamene anawapulumutsa mozizwitsa pa Nyanja Yofiira
Mfumu Davide anasankha amuna 4,000 kuti akhale oimba pa kachisi
Usiku woti afa mawa lake, Yesu ndi ophunzira ake anaimba nyimbo zotamanda Yehova
Kodi ndi pa zochitika ziti pamene ndingakhale ndi mwayi woimba nyimbo zotamanda Yehova?