CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 23-24
Musamatsatire Khamu la Anthu
Yehova anachenjeza mboni komanso oweruza milandu kuti asamatengeke ndi khamu la anthu kuti apereke umboni wonama kapena kuweruza mopanda chilungamo. Mfundo imeneyi ingatithandizenso pochita zinthu zambiri. Tikutero chifukwa chakuti nthawi zonse Akhristu akufunika kuyesetsa kuti asatengere maganizo komanso makhalidwe oipa am’dzikoli.—Aro 12:2.
N’chifukwa chiyani si nzeru kutsatira khamu la anthu pamene
tamva nkhani zopanda umboni kapena miseche?
tikusankha zovala, masitayilo a tsitsi kapena zosangalatsa?
tikuganizira kapena kuchita zinthu ndi anthu amtundu wina, chikhalidwe china kapena amene timasiyana nawo pa nkhani ya chuma?